Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/08 tsamba 1
  • Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 7/08 tsamba 1

Pindulani Pophunzira Buku la Yandikirani kwa Yehova

1 Mwezi wa August tidzayamba kuphunzira buku la Yandikirani kwa Yehova pa Phunziro la Buku la Mpingo. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tidzapindule kwambiri ndi phunzirolo? M’pofunika kukonzekera. Mutu uliwonse udzatenga milungu iwiri, ndipo tiziphunzira ndime zowerengeka chabe mlungu uliwonse. Zimenezi zidzakupatsani mpata wopereka ndemanga zochokera pansi pa mtima zimene munapeza pophunzira ndi posinkhasinkha nkhaniyo. Ndiponso, m’milungu imene tizikambirana mbali yomaliza ya mutu, tizipenda ndime zocheperapo kuti tikhale ndi nthawi yoona mbali yapadera ya bukuli.

2 Kuyambira mutu 2, chakumapeto kwa mutu uliwonse kuli bokosi la mutu wakuti “Mafunso Owasinkhasinkha.” Atamaliza kuphunzira ndime yomaliza m’mutu uliwonse, woyang’anira phunziro la buku azikambirana ndi kagulu kake za m’bokosilo. Aziwalimbikitsa kupereka ndemanga zawo, kutchula mfundo zabwino zimene anapeza posinkhasinkha Malembawo. (Miy. 20:5) Kuwonjezera pa mafunso amene ali m’bokosimo, iye nthawi zina angafunse mafunso onga akuti: “Kodi mfundo imeneyi ikutiuza chiyani za Yehova? Kodi ikukhudza motani moyo wathu? Kodi tingaigwiritse ntchito motani kuthandizira ena?” Cholinga chake chikhale kuwalimbikitsa kupereka ndemanga zochokera pansi pa mtima, osati kuwayesa nzeru pa mfundo zosafunika kwenikweni.

3 Buku la Yandikirani kwa Yehova n’losiyana kwambiri ndi mabuku ena. Inde, mabuku onse a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amalemekeza Yehova, koma buku ili lakonzedwa ndi cholinga chofotokoza makhalidwe a Yehova basi. (Mat. 24:45-47) Komatu ndiye tikuyembekeza kudzasangalala! Tidzapindula kwambiri pophunzira mwakuya za umunthu wa Yehova. Phunziro limeneli lidzatithandizetu kuyandikira kwambiri kwa Atate wathu wa kumwamba, ndipo tidzakhaletu ogwira mtima pothandiza ena kuchita chimodzimodzi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena