Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/08 tsamba 1
  • Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Kuchita Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Kuchita Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 8/08 tsamba 1

Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Kuchita Utumiki

1 Cholinga chathu chachikulu tikamachititsa maphunziro a Baibulo ndicho kupanga ophunzira atsopano otithandiza pa ntchito yophunzitsa ena. (Mat. 28:19, 20) Motero cholinga chathu si kungophunzitsa anthu kuti azidziwa Baibulo; koma kuwathandiza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuwakonzekeretsa kufotokoza chiyembekezo chawo kwa ena. (2 Akor. 4:13) Kodi tingachite zinthu ziti kuti tithandize ophunzirawo kukhala oyenerera kuphunzitsa ena?—2 Tim. 2:2.

2 Athandizeni Kukhala ndi Cholinga Chochita Utumiki: Mukangoyamba kuphunzira ndi munthu, muthandizeni kuzindikira kuti ‘kulengeza poyera chikhulupiriro’ ndi mbali ya kulambira koona. (Aroma 10:10) Ngakhale dzina lathu lakuti Mboni za Yehova, palokha limasonyeza kuti tiyenera kuuza ena za Yehova. Athandizeni kuona kuti si kuti zimene tikuwaphunzitsa n’zongoti ziwapulumutse iwo okha basi. Nawonso akadzayamba kuphunzitsa, adzathandiza anthu ena kukhala ndi mwayi wopeza chipulumutso.—1 Tim. 4:16.

3 Bwerezani Zimene Mwakhala Mukuwaphunzitsa: Kubwereza nthawi ndi nthawi zinthu zimene mwakhala mukuphunzira kumathandiza kwambiri. Kumathandiza wophunzirayo kukula mwauzimu chifukwa choonadi chimene wangophunzira kumenecho chimakhomerezeka m’maganizo ndi mumtima mwake. Mwachitsanzo, tonse tikudziwa mmene zimatithandizira poyankha mafunso obwereza amene amakhala m’Phunziro la Nsanja ya Olonda. Konzani mafunso osavuta ndiponso osazungulira kuti munthu amene mukumuphunzitsayo athe kuyankha kuchokera pansi pamtima.

4 Pobwerezapo mungathe kuyerekezera kuti wophunzirayo ali muutumiki. Mungatero pomufunsa mafunso kapena pofotokoza zinthu zimene timakumana nazo polalikira. Inuyo mukhale ngati mwininyumba ndipo iyeyo azikulalikirani. Muyamikireni pa zimene wachita bwino, ndipo muuzeni mfundo zina zimene zingam’thandize kuwonjezera luso lake. Njira imeneyi ingam’phunzitse kugwiritsira ntchito zimene waphunzira ndi kum’thandiza kuti azigwiritsira ntchito Baibulo mwaluso kwambiri.

5 Buku la Kukambitsirana: Onetsetsani kuti wophunzirayo ali ndi buku lake la Kukambitsirana, ndipo m’phunzitseni mmene angaligwiritsire ntchito. M’sonyezeni m’bukumo njira zoyambira kukambirana ndi munthu, kuyankha mafunso a Baibulo, kapena zoyenera kuchita akamatsutsidwa. Musonyezeninso njira zolankhulira kwa ena mogwira mtima. Buku limeneli lingam’thandize kuti asamadzikayikire, motero nthawi zambiri sangamachite mantha kulengeza uthenga wa Ufumu.

6 Musonyezeni Kuti Misonkhano ndi Yofunika Kwambiri: Cholinga cha misonkhano yampingo, makamaka Msonkhano wa Utumiki ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ndicho kutithandiza kuti tikhale okonzeka kuchita utumiki wakumunda. Pamisonkhanoyi timaphunzira mfundo zonse zofunika kwambiri polalikira, zomwe zimatchulidwa m’nkhani ndi m’zitsanzo za ofalitsa aluso. M’thandizeni kuona kuti misonkhano ndi yofunika kwambiri, ndipo chitani zimene mungathe pomuthandiza kuti azibwera ku misonkhano. Kufika ku misonkhano nthawi zonse kungam’thandize kukhala wophunzira weniweni wa Yesu.

7 Chinthu china chosafunika kuchinyalanyaza ndicho chitsanzo chanu. Mukamakonda kuchita nawo ntchito yolalikira nthawi zonse mumaonetsa kuti mumayamikira kwambiri choonadi. Zimenezi zimalimbikitsa wophunzirayo kuyesetsa kuchita chimodzimodzi posonyeza chikhulupiriro chake. (Luka 6:40) Zonsezi zingathandize munthu watsopanoyo kuyamikira kwambiri utumiki n’kumaona kuti ndi mwayi waukulu kuti iyeyo angathe kuchita nawo utumikiwo.—1 Tim. 1:12.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena