Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira August 11
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pemphani omvera kuti atchule nkhani za m’magazini atsopano zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Apempheni kuti afotokoze mmene angachitire pogawira magaziniwo mwa kugwiritsa ntchito nkhani zimene asankha. Kodi angafunse mafunso otani kuti ayambe kukambirana ndi munthu? Kodi ndi malemba ati m’nkhanizo amene angagwiritse ntchito? Kodi angawafotokoze bwanji kuti agwirizane ndi mayankho a mafunsowo? Pangani chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito njira zimene mwakambiranazo pogawira magazini.
Mph.15: Timafalitsa Uthenga Wabwino wa Zinthu Zabwino. Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndipo mkulu akambe nkhaniyi, yomwe yachokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2005, masamba 8-19, ndime 10-14. Auze omvetsera kuti anene mmene kumva uthenga wa Ufumu kunawalimbikitsira ndi kuwapatsa chiyembekezo.
Mph.20: “Kodi Mumagwiritsa Ntchito Nkhani Zonse za M’magazini Yogawira?”a Funsani wofalitsa mmodzi kuti anene zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo pogwiritsa ntchito nkhani zatsopano m’magazini yogawira ya Nsanja ya Olonda. Achite chitsanzo cha zinthu zimene zinachitikazo. Pogwiritsa ntchito mfundo za m’ndime yachiwiri, chitaninso chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro pogwiritsa ntchito nkhani yakuti “Zimene Tikuphunzira kwa Yesu,” imene ili mu Nsanja ya Olonda ya August 1.
Mlungu Woyambira August 18
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kumbutsani omvera kuti pobwera ku Msonkhano wa Utumiki mlungu wamawa adzatenge Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September ndiponso kuti akakonzekere kudzafotokoza ulaliki umene akufuna kudzagwiritsa ntchito.
Mph.15: Kuvala ndi Kudzikongoletsa Kwathu Kungalemekeze Yehova. Ikambidwe ndi mkulu. Popeza Yehova ndi Mulungu woyera, anthu ake ayenera kukhala aukhondo. (Eksodo 30:17-21; 40:30-32) Ngati timavala ndi kudzikongoletsa bwino, makamaka tikakhala muutumiki, timasangalatsa ndiponso kulemekeza Yehova. (1 Pet. 2:12) Koma tikalephera kuchita zimenezi ‘mawu a Mulungu amanyozedwa.’ (Tito 2:5) Fotokozani chitsanzo cha m’deralo kapena chimene chinalembedwa m’mabuku kapena magazini, chosonyeza mmene kuvala ndi kudzikongoletsa kunathandizira kuti anthu achite chidwi ndi choonadi.
Mph.20: “Konzekeretsani Ophunzira Baibulo Kuchita Utumiki.” Pokambirana ndime 4 ndi 5, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene mungathandizire wophunzira kukonzekera kukalalikira pakhomo. Wophunzirayo ayambe chitsanzo chake polankhula mawu ochepa chabe kenako n’kuwerenga Salmo 37:11. Mphunzitsiyo am’dule pakamwa n’kunena kuti: “Ine ndili kale ndi chipembedzo changa.” Wophunzirayo akusowa chonena. Onse akutsegula buku la Kukambitsirana, pa tsamba 18 ndi 19, n’kusankhapo yankho limodzi limene wophunzirayo akuona kuti sangavutike kulifotokoza. Kenako wophunzirayo akuyambanso kuchita chitsanzo chija ndipo akuyankha bwinobwino moti zimenezi zikumulimbikitsa kwambiri.
Mlungu Woyambira August 25
Mph 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndiponso mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera,” ndipo lengezani deti la tsiku la msonkhano wapadera wotsatira ngati ladziwika.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini a Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September. Kukambirana ndi omvetsera. Pambuyo pofotokoza mwachidule nkhani za mu magaziniwa, pemphani omvetsera kuti atchule nkhani zimene zingasangalatse anthu a m’gawo lanu. Kodi ndi funso ndi lemba liti limene angagwiritsire ntchito poyamba kukambirana nkhanizo ndi munthu? Chitani chitsanzo cha mmene tingagwiritsire ntchito njira imodzi yogawira magaziniwa pa njira zofotokozedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mkulu mmodzi achite chitsanzo chachidule cha zimene angachite pogawira magaziniwo. Asankhe nkhani imene iyeyo waona kuti ingakhale yoyenera m’gawo lanu.
Mlungu Woyambira September 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa August.
Mph.20: Tisawaiwale Ngakhale Amakhala Kwaokha. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2008, tsamba 25 mpaka 28. Tchulani mayina a abale ndi alongo a mumpingo wanu amene ali ku chipatala. Ngati palibe aliyense gwiritsani ntchito mfundo za m’nkhani ino polimbikitsa mpingo kuthandiza anthu amene akudwala kapena amene sakutha kuchita zinthu zina pampingo chifukwa cha thanzi lawo.
Mph.15: Yambitsani Phunziro la Baibulo Paulendo Woyamba mu September. Kukambirana ndi omvetsera. M’mwezi wa September uno, tigawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Yesetsani kukambirana ndi mwininyumba ndime zingapo za m’bukuli paulendo woyamba. Kambiranani mfundo zomwe zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo paulendo woyamba.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.