Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse mwa timabuku tamasamba 32 iti: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo woyamba. Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, athandizeni kuona mmene angapindulire nalo mwa kuwasonyeza mwachidule mmene timachitira phunziro la Baibulo. October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi, gawirani ndi kukambirana kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Zambiri za Baibulo? n’cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Kalendala ya 2009 ya Mboni za Yehova, ndiponso 2009 Yearbook of Jehovah’s Witnesses pa oda ya mwezi wotsatira. Zinthu zimenezi sizitumizidwa popanda kuitanitsa. Mungathe kuitanitsa kalendala ya Chichewa kapena ya Chingelezi koma Yearbook ilipo m’Chingelezi basi. Izi ndi zinthu zofunsira mwapadera motero musaitanitse ngati palibe ofalitsa amene achita kunena kuti akuzifuna. Zinthu zimenezi zisanafike zimalembedwa pa mpambo wolongedzera, pa mawu akuti “Zoyembekezeredwa.” Lengezani zimenezi kumpingo musanatumize fomu yoitanitsa mabukuwo. Ofalitsa asachedwe kulembetsa zinthuzi kwa m’bale wosamalira mabuku ndipo m’baleyo asachedwenso kuziitanitsa ku ofesi ya nthambi. Woyang’anira wotsogolera ayenera kuonetsetsa kuti zimenezi zikuchitikadi. M’pofunika kuchita zinthu zonsezi mwadongosolo, chifukwa mukadzapanda kuzilandira sipadzakhala njira ina yozitumizira kapena yozitengera msangamsanga ku ofesi ya nthambi. Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti mpingo waitanitsa zinthu zokhazo zimene udzagwiritsiredi ntchito.
◼ Mipingo isaitanitse Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku 2009 chifukwa mabuku amenewa tidzawatumiza ku mipingo yonse mogwirizana ndi kuchuluka komanso zinenero za Utumiki Wathu wa Ufumu. Komabe, ngati mpingo ukufuna mabuku owonjezera kapena a zinenero zina, lembani zimenezi pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Mulembe kuti: “Mabuku amene tikuitanitsawa ndi owonjezera pa mabuku amene mutitumizire.”
◼ Akulu akukumbutsidwa kutsatira malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991 pa tsamba 21-23 okhudza anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa amene akufuna kubwezeretsedwa.
◼ Kumbukirani izi: Popeza mwezi wa August ndi mwezi womalizira wa chaka chathu chautumiki, tikukupemphani kuti muonetsetse kuti mwapereka mwamsanga malipoti autumiki wa kumunda a mweziwo, kuphatikizapo malipoti alionse amene sanatumizidwe miyezi ya m’mbuyomo. Alembi tikukupemphani kuti mutolere ndi kutumiza mwamsanga malipoti a mwezi wa August ndi ena onse a miyezi ya m’mbuyo. Zikomo kwambiri chifukwa chotsatira malangizo ofunikawa.
◼ Ma DVD Atsopano Amene Alipo:
Album for The Watchtower Announcing Jehovah’s Kingdom—2008 (dvcw08)—American Sign Language
◼ Pali Ma DVD Atsopano Otsatirawa, Okhala ndi Zinenero Zambiri:
Warning Examples for Our Day and Respect Jehovah’s Authority (dvwra)—Chiarabu, Chidatchi, Chingelezi, Chimalagase, Chipwitikizi (cha ku Brazil), Chipwitikizi (cha ku Ulaya) ndi Chisipanishi (Zinenero zonsezi zili pa DVD imodzi)
(Zapitirizidwa patsamba 3)
Zilengezo (Zachokera patsamba 2)