Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 25, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 7 mpaka August 25, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife ololera pamene tikulalikira choonadi? (Afil. 4:5) [be-CN tsa. 251 ndime 3]
2. Kodi zimene Paulo anachita pamene ankalankhula ndi Agiriki ku Areopagi zingatithandize bwanji tikamalalikira kwa anthu amene saona kuti Baibulo ndi lofunika pamoyo wawo? (Mac. 17:22, 23) [be-CN tsa. 252 ndime 1-2]
3. Kodi tingasonyeze bwanji kulolera ngakhale tikudziwiratu kuti zimene munthu amene tikulankhula naye akunena si zoona? [be-CN tsa. 252 ndime 5 mpaka 253 ndime 1]
4. Tikamayesetsa kuti tilankhule ndi ena m’njira yokopa, kodi tiyenera kukumbukira chiyani? [be-CN tsa. 255 ndime 3, bokosi]
5. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji luso la kuzindikira pofuna kuwafika pamtima omvetsera athu? (Miy. 20:5) [be-CN tsa. 258 ndime 1-5]
NKHANI NA. 1
6. Kodi alongo ayenera kuganizira chiyani pokonzekera nkhani mogwirizana ndi mtundu wa makambirano? [be-CN tsa. 44 ndime 5 ndi 6]
7. Pokamba mfundo zazikulu za m’Baibulo kodi m’bale ayenera kuyesetsa kuchita chiyani? (Neh. 8:8) [be-CN tsa. 47 ndime 2 ndi 3]
8. Kodi m’bale ayenera kukamba motani nkhani yokhala ndi chitsanzo kapena yokhala ndi athu oti awafunse mafunso ya mu Msonkhano wa Utumiki? [be-CN tsa. 49 ndime 5]
9. N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti atumiki odzipereka a Yehova azikhala ndi zolinga zauzimu? [od-CN tsa. 117 ndime 1]
10. Kodi m’bale wokamba nkhani ya onse angachite chiyani pofuna kuonetsetsa kuti mfundo za m’nkhani yake n’zochokera m’Baibulo? (Mac. 17:2, 3) [be-CN tsa. 52 ndime 6 mpaka tsa. 53 ndime 2]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. N’chifukwa chiyani woyang’anira ndende wa ku Filipi anafuna “kuti adziphe”? (Mac. 16:25-27) [w90-CN 5/15 tsa. 25, bokosi]
12. Ngakhale kuti Apolo anali ndi “mphatso ya kulankhula” ndiponso “wodziwa bwino Malemba,” n’chifukwa chiyani Purisikila ndi Akula anafunika “kum’fotokozera njira ya Mulungu molondola koposerapo”? (Mac. 18:24-26) [w96-CN 10/1 tsa. 20 ndime 4 ndi 5]
13. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani ponena kuti Saulo ‘ankachita ngati nyama yoponya zidyali pa zisonga zotosera’? (Mac. 26:14) [w03-CN 10/1 tsa. 32]
14. Kodi uchimo “unadzutsidwa” motani ndi lamulo la Mulungu kwa Aisiraeli? (Aroma 7:8, 11) [w08-CN 6/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Aroma”]
15. Kodi ‘timaunjika [motani] makala a moto pamutu’ pa mdani wathu? (Aroma 12:20) [w08-CN 6/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Aroma”]