Kukonzekera Nkhani ya Wophunzira mu Sukulu
NKHANI iliyonse m’sukulu imapereka mwayi wokuthandizani kupita patsogolo. Dziperekeni ndi mtima wonse, ndipo kupita kwanu patsogolo kudzaonekera kwa inu mwininu ndi kwa ena. (1 Tim. 4:15) Sukuluyi idzakuthandizani kukulitsa maluso anu.
Kodi mumachita mantha kulankhula pamaso pa mpingo? Zimenezo n’zachibadwa, ngakhale kuti mwakhala m’sukuluyi nthaŵi yaitali. Komabe, zilipo njira zimene mungachepetsere mantha anu. Kunyumba, khalani ndi chizoloŵezi choŵerenga mokweza kaŵirikaŵiri. Pamisonkhano yampingo, yankhani kaŵirikaŵiri, ndipo ngati ndinu wofalitsa, pitani nawoni nthaŵi zonse mu utumiki wa kumunda. Njira zimenezi zidzakuthandizani kuzoloŵera kulankhula pamaso pa anthu. Kuwonjezera apo, konzekerani nkhani zanu za wophunzira nthaŵi ikalipo, ndipo yesezani kuzikamba motulutsa mawu. Kumbukirani kuti muzikalankhula pamaso pa omvera aubwenzi. Ndipo musanakambe nkhani ina iliyonse, pempherani kaye kwa Yehova. Iye amapereka mokondwa mzimu woyera kwa atumiki ake amene amaupempha.—Luka 11:13; Afil. 4:6, 7.
Musayembekezere kuchita zodabwitsa. Kukhala wokamba bwino nkhani ndi mphunzitsi waluso kumatenga nthaŵi. (Mika 6:8) Ngati munalembetsa posachedwa m’sukuluyi, musayembekezere kuti mukakamba nkhani yothyakuka bwino kuyamba n’kuyamba. M’malo mwake limbikirani mfundo imodzi ya chilangizo cha kalankhulidwe panthaŵi imodzi. Ŵerengani ndi kumvetsetsa gawo la m’buku lino limene limafotokoza mfundo ya chilangizo imeneyo. Ngati n’kotheka, chitani zimene zandandalikidwa pambali yakuti “Zochita.” Zimenezi zidzakuthandizani kuzoloŵera luso limenelo la kalankhulidwe musanakakambe nkhani yanu kumpingo. Kumbukirani, kupita patsogolo kumadza ndi kudekha.
Kukonzekera Mbali ya Kuŵerenga
Kukonzekera kuŵerenga pamaso pa anthu kumalira zambiri, kusiyana ndi kungotchula mawu mmene awalembera m’nkhaniyo. Yesetsani kumvetsetsa zimene mukuŵerengazo. Mukangolandira mbali imeneyo, iŵerengeni mobwerezabwereza ndi cholinga chimenecho. Yesani kumvetsetsa mfundo ya sentensi iliyonse ndi lingaliro limene akulimveketsa m’ndime iliyonse. Mukatero mudzamveketsa malingalirowo molondola ndi mzimu wake. Ngati n’kotheka, yang’anani mu mtanthauzira mawu, kuti mudziŵe katchulidwe ka mawu osazoloŵereka. Imvetseni bwino nkhaniyo. Makolo angafunikire kuthandiza ana awo kuti achite zimenezi.
Kodi mumapatsidwa mbali zoŵerenga Baibulo kapena ndime m’nkhani za mu Nsanja ya Olonda? Ngati zoŵerengazo zilipo pamakaseti m’chinenero chanu, mungathandizike kwambiri ngati mumvetsera kaŵerengedweko ndi kusamala zinthu ngati katchulidwe ka mawu, kalankhulidwe, mmene amatsindikira mawu, komanso kakwezedwe ndi katsitsidwe ka mawu. Ndiyeno yesani maluso ameneŵa pakuŵerenga kwanu.
Mukayamba kukonza nkhani yanu, onetsetsani kuti mwaŵerenga ndi kumvetsetsa phunziro limene limafotokoza luso la kulankhula limene mwauzidwa kuti mukonzekere. Ngati n’kotheka, ŵerenganinso phunzirolo mutayeseza kangapo kuŵerenga momveka mbali imene mwapatsidwayo. Yesetsani kugwiritsa ntchito malangizo onse olembedwawo.
Maphunziro ameneŵa adzakuthandizani kwambiri mu utumiki wa kumunda. Pamene muli mu ulaliki, mumakhala ndi mwayi wochuluka woŵerenga kwa anthu ena. Popeza kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yosintha miyoyo ya anthu, m’pofunika kuti muziwaŵerenga bwino. (Aheb. 4:12) Musayembekezere kudziŵa maluso onse a kaŵerengedwe pamene mwaŵerenga kamodzi kapena kaŵiri kokha ayi. Mtumwi Paulo analembera mkulu wa mumpingo komanso wodziŵa kuti: “Usamalire kuŵerenga.”—1 Tim. 4:13.
Kukonzekera Nkhani Yokambirana
Mukapatsidwa nkhani yokambirana m’sukulu, kodi mungaikonzekere motani?
Pali zinthu zitatu zofunika kuziganizira: (1) nkhani imene mwapatsidwa, (2) mtundu wake wa makambirano ndi munthu amene mudzakambirana naye, ndipo (3) mfundo ya chilangizo imene munapatsidwa kuti mukonzekere.
Muyenera kusanja mfundo pankhani imene mwapatsidwa. Koma musanafike patali, lingalirani mofatsa za mtundu wa makambirano anu ndi munthu amene mudzakambirane naye. Zimenezi n’zofunika chifukwa zidzakhudza kwambiri mfundo zimene mudzafotokoze ndi njira imene mudzazifotokozere. Kodi makambirano anu adzakhala a mtundu wanji? Kodi adzakhala osonyeza mmene mungalalikire uthenga wabwino kwa munthu amene mumam’dziŵa kale? Kapena adzakhala osonyeza mmene mungachitire pokambirana ndi munthu kwa nthaŵi yoyamba? Kodi munthuyo ndi wamkulu kapena wamng’ono kwa inu? Kodi angakhale ndi maganizo otani pankhani imene mukufuna kukambirana naye? Kodi angakhale akudziŵa zochuluka motani pankhaniyo? Kodi cholinga chanu n’chiyani pamapeto pa makambiranowo? Mayankho pa mafunso ameneŵa adzakuthandizani mmene mungakonzekerere.
Kodi mfundo za nkhani imene mwapatsidwa mungazipeze kuti? Pamasamba 33 mpaka 38 a buku lino, tafotokozapo “Mmene Mungafufuzire.” Ŵerengani gawo limenelo ndi kugwiritsa ntchito zida zofufuzira zimene mungapeze. Kaŵirikaŵiri mudzapeza mfundo zochuluka kuposa zimene mungazigwiritse ntchito. Ŵerengani mokwanira kuti mupeze mfundo zoyenerera kwambiri. Komabe mmene mukutero, kumbukirani mtundu wa makambirano a nkhani yanu komanso munthu amene mudzakambirane naye. Lembani mzera kunsi kwa mfundo zoyenera kugwiritsa ntchito.
Musanasankhe komaliza mfundo zoyenerera ndi kuiyala nkhani yanu, ŵerengani mofatsa nkhani yofotokoza luso la kulankhula limene munapatsidwa kuti mulikonzekere. Kugwiritsa ntchito kwanu luso limenelo pankhani yanu ndiko chimodzi mwa zifukwa zazikulu zokupatsirani nkhaniyo.
Mukakakamba mfundo zanu m’nthaŵi imene mwapatsidwa, mudzakhala ndi mpata wabwino wokamba mawu omaliza, chifukwa adzakupatsani chizindikiro chosonyeza kuti nthaŵi yanu yakwana. Komabe, pamene muli mu utumiki wa kumunda, nthaŵi siikhala nkhani yaikulu. Choncho pamene mukukonzekera, ganizirani za nthaŵi, koma makamaka samalani za luso la kuphunzitsa.
Mawu Pang’ono za Mtundu wa Makambirano. Pendani njira zosonyezedwa patsamba 82, ndipo sankhanipo imodzi imene ingakhale yogwira mtima kwa inu mu ulaliki komanso imene ingakuthandizeni kugwiritsa ntchito bwino mfundo za nkhani imene mwapatsidwa. Ngati mwakhala m’sukuluyi kwa nthaŵi yotalikirapo, umenewu ukhale mwayi wanu wakuti muchite khama ndi kuwonjezera maluso ena mu ulaliki.
Ngati woyang’anira Sukulu ya Utumiki akusankhirani mtundu wa makambirano, landirani musaope. Makambirano ambiri a m’nkhani amakhala ochita ulaliki. Ngati simunachitepo ulaliki umene akupatsaniwo, funsirani kwa ofalitsa amene anauchitapo. Ngati n’kotheka, yesani kukambirana nkhani imene mwapatsidwayo m’njira yofanana ndi imene mudzagwiritse ntchito m’sukulu. Zimenezi zidzakuthandizani kupeza cholinga chenicheni cha kuphunzira kwanu.
Pamene Nkhani Yanu Ili Yokamba Nokha
Ngati ndinu mwamuna, mungapatsidwe nkhani yaifupi yokaikamba ku mpingo. Pokonzekera nkhani ngati zimenezi, mfundo zoyambirira kuziganizira n’zofanana ndi zimene tafotokoza m’nkhani zokambirana za wophunzira. Kusiyana kwakukulu kumene kulipo ndiko omvera ndi kakambidwe basi.
Kumakhala bwino kukonzekera m’njira yoti aliyense mwa omvera akapindule. Ambiri omwe amakhalapo ndi oti amadziŵa kale ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Angakhale akudziŵapo zambiri pa nkhani imene munapatsidwa kuti muikambe. Ganizirani zimene akuzidziŵa kale m’nkhaniyo. Yesetsani kupeza njira imene mungawapindulitsire nayo. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani yangayi ndingaigwiritse ntchito motani kuti ndizamitse chidziŵitso changa ndi cha omvera anga pa makhalidwe a Yehova? Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuzindikira chifuniro cha Mulungu? Kodi nkhaniyi ingatithandize motani kupanga zosankha zanzeru m’dzikoli lodzaza zilakolako za thupi?’ (Aef. 2:3) Kupeza mayankho okhutiritsa pa mafunso ameneŵa kumalira kufufuza. Pamene mukugwiritsa ntchito Baibulo, musangoŵerenga malemba n’kuthera pomwepo. Lingalirani pamalembawo, ndipo sonyezani mmene akuperekera umboni pa mfundo zanu. (Mac. 17:2, 3) Musakhale ndi mfundo zochuluka kwambiri. Zifotokozeni m’njira yosavuta kuzikumbukira.
Pokonzekera muyenera kuganiziranso za mmene mukalankhulire. Mfundo imeneyi musaichepetse. Yesezani kukamba nkhani yanu motulutsa mawu. Khama limene mumaika pa kuŵerenga ndi kugwiritsa ntchito malangizowo pa maluso osiyanasiyana a kalankhulidwe lidzakuthandizani kwambiri kupita patsogolo. Kaya mwayamba posachedwa kukamba nkhani kapena munayamba kale, konzekerani bwino kuti mukalankhule mwachidaliro ndi mzimu wake wa nkhaniyo. Pamene mukukamba nkhani iliyonse m’sukulu, kumbukirani cholinga chogwiritsira ntchito mphatso ya kulankhula yochokera kwa Mulungu, kutamanda Yehova.—Sal. 150:6.