Phunziro 8
Phindu la Kukonzekera
1-5. Kodi kukonzekera kumapindulitsa ndani, ndipo chifukwa chiyani?
1 Paulo, mtumwi wa kwa amitundu, analimbikitsa mtumiki mnzake Tito kupitiriza ‘kukumbutsa [Akristu] . . . kukhala okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino.’ (Tito 3:1) Zimenezo zinatanthauza kuti iwo anayenera kukhala okonzeka m’maganizo ndi m’kachitidwe kam’tsogolo.
2 Ndithudi, kukonzekera n’kopindulitsa pa ntchito ina iliyonse yateokalase. Zoona, nthaŵi yoyamba imene muchita ntchito ina, mumafunikira kukonzekera kwambiri chifukwa ntchitoyo n’njatsopano kwa inu. Koma pamene chidziŵitso chanu chiwonjezeka, mudzapeza kuti mumatapanso nzeru pa zomwe munaphunzira nthaŵi ya m’mbuyo kuphatikiza pa chidziŵitso chimene mwangochipeza tsopano. Komabe, zilibe kanthu kuti nkhaniyo mwaikambapo kangati m’mbuyomu, kukonzekera kumakhalabe kopindulitsa nthaŵi zonse.
3 Kukonzekera n’kofunika, osati kwa amene apatsidwa nkhani okha, komanso kwa aliyense wofuna kukhala mlaliki wokhoza bwino wa uthenga wabwino. Mutachita nawo ntchito ya kunyumba ndi nyumba kwa miyezi yambiri kapena zaka zambiri, mumapeza kuti simufunikiranso nthaŵi yochuluka kwambiri yokonzekera nthaŵi iliyonse pamene mupita mu ulaliki. Komabe mukamakonzekera, nthaŵi zonse mudzakhala wogwira mtima. Chimodzimodzi ndi kuchititsa phunziro la Baibulo. Phunziro la Baibulo loyamba limene munachititsa linafuna kukonzekera kwambiri. Komabe ngakhale kuti tsopano nkhaniyo mwaiphunzira mobwerezabwereza, mudzaiphunzitsa bwino kwambiri ngati muibwereramo muli ndi wophunzira wanuyo m’maganizo. N’chimodzimodzinso polankhula papulatifomu. Chidziŵitso chimene mwakundika pazaka zonsezi n’chothandiza kwambiri. Koma pamene mwadziŵa pasadakhale kuti mudzakamba nkhani, musayerekeze n’komwe kuikamba chosakonzekera.
4 Ponena za Sukulu ya Utumiki Wateokalase, kukonzekera n’kopindulitsa kwambiri kwa ife tonse. Wophunzira aliyense ali ndi kope la ndandanda ya sukulu ndipo atha kuonapo machaputala a Baibulo kapena nkhani zina zodzakambidwa tsiku lililonse. Choncho amene amakonzekera kwambiri pasadakhale, ndiwo amapindulanso kwambiri ndi sukuluyo. Kulephera kuzindikira phindu la kukonzekera pasadakhale kungakumanitseni mapindu enieni ambiri.
5 Kukonzekera kumatenga nthaŵi yochuluka, koma mapindu ake amakhala oposerapo. Sikumangothandiza kuchita bwino pa kubwereramo kwapakamwa, komanso kumakuthandizani kupeza maganizo a Yehova ndi kukulitsa kuzindikira kwanu “chinenero choyera” cha choonadi. (Zef. 3:9, NW) Kuti kukonzekera sukulu pasadakhale kukhale chizoloŵezi chanu, mungalinganize kuti kuŵerenga ndi kuphunzira koteroko kuzichitidwa limodzi ndi apabanja lanu kapena limodzi ndi mabwenzi anu ena. Zoona, aliyense wolembetsa m’sukulu ali ndi mwayi wokamba nkhani, choncho ndi bwino kuti tikupatseni malingaliro ena a kakonzekeredwe ka nkhanizo.
6. Kodi tiyenera kukonzekera motani gawo loŵerenga pa sukulu yateokalase?
6 Nkhani zoŵerenga. Nthaŵi ndi nthaŵi nkhani zoŵerenga zimasonyezedwa pandandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Kuti mukonzekere nkhani yotero, iŵerengeni mosamala. Zoloŵerani matchulidwe a mayina ndi mawu ovuta. Yesezani mofuula kuti mukhoze kuŵerenga nkhaniyo monga mukungolankhula mwachibadwa, mosadodoma komanso mosalakwitsa mawu. Ndiponso samalani kuti mudzaŵerenge nkhaniyo m’nthaŵi yake yoperekedwa.
7-11. Pokonza nkhani kuchokera m’nkhani yofalitsidwa kale, kodi ndi zinthu ziti zofunika kuzikumbukira kuti tisankhe mfundo zofunikira?
7 Kukonza nkhani kuchokera m’nkhani yofalitsidwa kale. Choyambirira kuchita ndi nkhani yoteroyo ndicho kuŵerenga nkhani yofalitsidwayo mosamalitsa. Chongani mfundo zazikulu kapena lembani autilaini yachidule ya mfundo zazikulu papepala lapadera. Pezani malingaliro akulu ofotokozedwa. Nanga tsopano ndi mfundo ziti zimene mudzasankha, popeza mwina pali zambiri kuposa zimene mungazifotokoze m’nthaŵi yoperekedwayo? Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kusankha mfundo zofunika: (1) Omvetsera anu ndi mkhalidwe wa kumene muliko, ngati mkhalidwewo ungathandize kuona mmene nkhaniyo ingakambidwire mogwira mtima, ndiponso (2) mutu wa nkhani yanuyo ndi kusonyeza mmene mfundo zake zingagwirire ntchito.
8 Poganizira omvetsera anu, mudzafuna kusankha mfundo m’nkhani yofalitsidwa kaleyo zimene adzazikonda ndi zowapindulitsa. Ngati ndime zina m’nkhani yofalitsidwayo zioneka zokhwimirapo kwa omvetserawo, sumikani maganizo pa ndime zina. Ndiponso, malemba angapo okha amene musankha adzamveketsa chifukwa cha zinthu zimene inu mukunena. Ngati muganizira omvetsera anu, simudzayesa kufotokoza mfundo zambirimbiri, chifukwa ngati muthamanga nazo, phindu lake lenileni lidzatayika. Chifukwa chake, ndi bwino kukamba bwinobwino mfundo zoŵerengeka.
9 Ponena za nkhani zambiri za wophunzira, n’kopindulitsa kukhala ndi mkhalidwe wakutiwakuti wokhudzana ndi nkhani yanuyo. Mkhalidwe wake ungakhale monga kulankhula ndi munthu wina m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba; kapena ungakhale kuyankha funso paulendo wobwereza; kapenanso umboni wa mwamwayi. Mungaikambenso monga ngati munali kufotokozera nkhaniyo mmodzi wa ana anu. Iliponso mikhalidwe ina imene mungaigwiritse ntchito. Chachikulu chofunika n’chakuti mkhalidwewo ugwirizane ndi zochitika zenizeni. Choncho lingalirani mosamalitsa za mkhalidwe wogwirizana ndi nkhani yanu. Funsirani kwa ofalitsa ena, mwina angakhale ndi malingaliro ena abwino kwambiri.
10 Kodi mwasankha mutu wa nkhani wotani ndipo mudzazifotokoza motani mfundo zake? Sankhani mfundo kuchokera m’nkhani yofalitsidwayo. Siyani mfundo zimene sizikuchirikiza kwenikweni mutu wanu wa nkhani ndi cholinga cha nkhani yanu. Kwenikweni, malingaliro ambiri ofunikira kuwafotokoza ali kale m’nkhaniyo, choncho ndi bwino kumamatira pazimenezo m’malo moyesa kulowetsamo mfundo zochuluka zakunja kwa nkhaniyo. Komabe, sikuti fanizo loyenerera silingagwiritsidwe ntchito, kapena mfundo ina imene ingathandize omvetsera anu kuzindikira phindu la nkhaniyo. Pamene kuli kotheka, tanthauzirani mfundozo kwa omvetsera anu kuti onse apeze phindu lalikulu kwenikweni.
11 Mutasankha mutu wa nkhani yanu ndi mkhalidwe wogwirizana ndi nkhaniyo, mungapeze kuti ndime zina za nkhani yosindikizidwayo sizikugwirizana bwino ndi nkhani yanu. Inu simudzangogwiritsa ntchito malingaliro onse a m’ndime iliyonse. M’malo mwake chitani ichi: Yesani kusankha mutu wa nkhani ndi mkhalidwe zimene zidzakulolani kugwiritsa ntchito mbali yaikulu ya nkhani yanu.
12. Kodi tingakonze motani nkhani kuchokera pa mndandanda wa malemba umene tapatsidwa?
12 Kukonza nkhani kuchokera pa mndandanda wa malemba. Nthaŵi zina mungapatsidwe mndandanda wa malemba, mwina kuchokera m’kabuku ka Mpambo wa Nkhani kapena m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Pamenepo cholinga chanu ndicho kukonza nkhani pa malemba amenewa, kaya nkhani yokaikamba kapena ulaliki wa m’munda. Ngati pa mndandandawo pali malemba ochuluka moti simungathe kuwafotokoza m’nthaŵi yoperekedwayo, sankhani okhawo amene mungawafotokoze. Musayese kugwiritsa ntchito ochuluka amene simungathe kuwafotokoza bwino m’nthaŵiyo. Ndiyeno pendani lemba lililonse limene mudzagwiritsa ntchito. Pezani chifukwa chanu choligwiritsira ntchito. Konzani nkhaniyo mwa njira yoti mawu anu oyamba ofotokozera lemba lililonse agwirizane ndi chifukwa chanucho choliŵerengera. Komanso kaŵerengedwe kanu ka lembalo kayenera kugogomeza mbali yake yofunika kwambiri. Mapeto ake, omvetsera adzamvetsa mfundo yaikulu ya lembalo.
13-15. Kodi ndi masitepe otani amene tingatsatire pokonza nkhani pamene tangopatsidwa mutu wake popanda nkhani ina yofalitsidwa monga maziko a nkhani yathu?
13 Pamene mwapatsidwa mutu wokha wa nkhani. Nthaŵi zina, kaya pa Sukulu ya Utumiki Wateokalase, pamsonkhano wautumiki kapena pamisonkhano ina, angakupempheni kukamba nkhani atakupatsani mutu wokha wa nkhani. Sadzanena mwachindunji kuti mukakonzekere nkhani yakutiyakuti monga maziko a nkhani yanu. Zikakhala choncho nayi njira imene mungaitsate: Fufuzani m’maganizo mwanu kenaka lembani mfundo zimene mukuona kuti zikakhala zoyenera kuzifotokoza. Sitepe loyamba limenelo n’lofunika kwambiri. Ichi n’chimene chidzasonyeza kaya nkhaniyo idzakhala yokonzedwa mwatsopano, kapena yangokhala kubwereza malingaliro a anthu ena. Kungaletsenso kufufuza ndi kuŵerenga kopanda cholinga, pakuti kudzapangitsa kufufuza kwanu kukhala kolunjika pa nkhani imodzi. Kuwonjezera pamenepo, mudzakamba nkhani m’njira yanuyanu osati ya wina yosagwirizana ndi kalankhulidwe kanu kachibadwa. Kungakhalenso kothandiza kulankhula za nkhani yanuyo ndi anthu achikulire. Iwo angakhale ndi malingaliro ena abwino a mmene mungafutukulire mutu wa nkhaniwo.
14 Ndiyeno mumakhala wokonzekera kuwonjezera chidziŵitso chanu mwa kufufuza m’Baibulo ndi mabuku ena mothandizidwa ndi konkodansi ndi ma indekisi a Sosaite. Kaŵirikaŵiri mutha kupeza zochuluka m’buku lililonse limene muligwiritsa ntchito pofufuza mwa kupenda choyamba mndandanda wa mitu yam’kati. Ndiyeno pendani cholozera mitu ya nkhani kuti muone kumene mungapeze nkhani imene ingakhale yokuthandizani. Kusankha bwino kudzakuthandizani kusawononga nthaŵi yochuluka. Poŵerenga pamakhala ngozi yotengeka maganizo ndi mfundo zina zosangalatsa koma zosagwirizana ndi mutu wa nkhani yanu. Peŵani mfundo zimenezo mwa kungoŵerenga nkhaniyo mwachisawawa, kwinaku mukumachonga zigawo zokhazo zimene mutha kuzigwiritsa ntchito. Chimene muyenera kuchita kaŵirikaŵiri ndicho kudziŵa chiganizo kaya kuti sentensi yokhala ndi mfundo yaikulu ya m’ndime iliyonse ndiyeno ŵerengani ndime zokhazo zimene muona kukhala zoyenera kuti muzigwiritse ntchito.
15 Pokhala ndi malingaliro anuanu limodzi ndi aja omwe mwasankha m’zofalitsa zina, tsopano muli wokonzekera kusankha mfundo zabwino kwambiri zimene mungazifutukule m’nthaŵi imene mwapatsidwa. Posankha mfundo zofunika pofufuza, dzifunseni mafunso onga aŵa: Kodi mfundoyi imagwiradi ntchito? Kodi n’njokondweretsa? Kodi idzagogomezera mutu wankhani yanga?
16, 17. Kodi ndi malingaliro otani amene aperekedwa ponena za kulemba notsi?
16 Kulemba notsi. Pokonzekera ndi pofufuza nkhani ina iliyonse yoti mudzakambe payenera kukhala njira yosungira mfundo zazikulu zimene mukuzifutukula. Ophunzira ena apeza kukhala kothandiza kugwiritsa ntchito makadi aang’ono kapena timapepala, akumalemba pa khadi lililonse mfundo zoti akazigwiritse ntchito m’nkhani yawo.
17 Notsizo zingakhale zachidule kwambiri, zongokukumbutsani mfundozo. Ubwino wa notsi zachidule n’ngwakuti nkhaniyo mumaikamba mwachibadwa, osati kuumirira pa mawu kapena ziganizo zobwerekedwa kwa wina. Lembani magwero a mfundo zanuzo kuti mudzakhoze kupezanso tsamba ndi ndime zitakhala zofunika. Lembaninso lemba lililonse lokhala ndi mfundo yaikulu monga maziko a nkhani yanu. Ubwino wina wogwiritsa ntchito makadi kapena timapepala ndi wakuti mutha kuwonjezapo tatsopano ndi kuchotsapo tinato pokonzekera nkhani yanu, popanda kuyambanso kulemba mwatsopano.
18. N’chifukwa chiyani timafuna kukhala anthu okonzekera?
18 Anthu okonzekera. Ngati pangakhale chizoloŵezi chonyalanyaza kukonzekera kunyumba mutapatsidwa gawo lateokalase, mungachite bwino kukumbukira kuti, kukonzekera n’kofunika kwambiri kwa aja ofuna chiyanjo cha Yehova. Mwachitsanzo, kumbukirani kuti, Yohane Mbatizi anapatsidwa ntchito ya ‘kukonzekeretsera Yehova anthu okonzekera.’ (Luka 1:17, NW) Aisrayeli “okonzekera” amenewo analola kuumbidwa ndi Yehova mwa zochita zake ndi iwo kotero kuti anakhala okhoza kuchita ntchito imene Iye anali atawakonzera. Zili chomwecho mwa ifenso: Mwa kuchita khama ndi Sukulu ya Utumiki Wateokalase komanso kukonzekera bwino nkhani zathu, timadzilola kuumbidwa ndi pologalamu imeneyi ya maphunziro imene Yehova wapereka. Mwakutero ifenso tidzakhala okonzekera kuchita ntchito yogwira mtima monga atumiki ake a Mulungu.