Kukonzekera Nkhani Zokambira Mpingo
SUKULU ya Utumiki wa Mulungu inakonzedwa ndi cholinga chopindulitsa mpingo wonse. Nkhani zopindulitsa zimakambidwanso pamisonkhano ina yampingo ndi pamisonkhano ikuluikulu. Mukapatsidwa gawo pamisonkhano imeneyi, dziŵani kuti mwapatsidwa udindo waukulu kwambiri. Mtumwi Paulo analimbikitsa woyang’anira wachikristu Timoteo kuti asamalire chiphunzitso chake mosalekeza. (1 Tim. 4:16) Amene amafika pamisonkhano yachikristu amakhala atapatula nthaŵi yofunika kwambiri—ndipo ena amakhala atavutikirapo kwambiri—chonsecho kuti adzalandire malangizo pankhani zokhudza unansi wawo ndi Mulungu. Kupereka malangizo oterowo ndi mwayi wosaneneka! Kodi mungausamalire bwino motani?
Mfundo Zazikulu za Kuŵerenga Baibulo
Mbali imeneyi ya sukulu imachokera pa kuŵerenga Baibulo kwa mlungu uliwonse. M’pofunika kwambiri kuunika mmene mfundozo zimatikhudzira lerolino. Monga momwe timaŵerengera pa Nehemiya 8:8, Ezara ndi anzake aja anaŵerengera anthu Mawu a Mulungu, akumawafotokozera, ‘nawatanthauzira,’ ndi kuwathandiza kumvetsa mawuwo. Pamene mukamba mfundo zazikulu za m’Baibulo, mumakhala ndi mwayi wakuchita zofananazo.
Kodi mungaikonzekere motani nkhani imeneyi? Ngati n’kotheka, ŵerengani gawo la Baibulo limene mwapatsidwalo kukali mlungu umodzi kapena kuposerapo. Kenako ganizirani za mpingo wanu ndi zosoŵa zake. Musaiŵale kuipempherera. Kodi ndi uphungu uti, ndi zitsanzo ziti, ndi mfundo za makhalidwe abwino ziti m’gawo limeneli la Mawu a Mulungu zimene zingathandize pa zosoŵa zimenezo?
Apanso kufufuza n’kofunikira. Mungagwiritse ntchito mlozera nkhani wa kumapeto kwa chaka wa mu Nsanja ya Olonda. Mwa kufufuza zimene zinafalitsidwa pamavesi amene mwasankhawo, mungapeze mfundo zina zounika bwino nkhaniyo, mafotokozedwe a maulosi okwaniritsidwa, mfundo zimene nkhani zina zimaunika zokhudza Yehova, kapena malongosoledwe a mfundo za makhalidwe abwino. Musalembe mfundo zambiri. Ikani maganizo pa mavesi oŵerengeka chabe amene mwasankha. Ndi bwino kulemba mfundo zoŵerengeka ndi kuzikamba bwino.
Nkhaniyi imaphatikizaponso kupempha omvera kuti alankhulepo mmene apindulira ndi kuŵerenga Baibulo kwa mlunguwo. Kodi anapeza mfundo zotani zimene zingawathandize paphunziro lawo laumwini ndi paphunziro la banja, kapena mu ulaliki wawo kapenanso m’njira zina pamoyo wawo? Ndi makhalidwe otani a Yehova amene anaona m’zochitika za pakati pa Yehova ndi anthu osiyanasiyana, komanso mitundu ya anthu yosiyanasiyana? Kodi omverawo anaphunzirapo chiyani chimene chalimbikitsa chikhulupiriro chawo ndi kuzamitsa chiyamikiro chawo kwa Yehova? Musataye nthaŵi ndi mfundo zovuta kumva zosafunikira kwenikweni. Gogomezani makamaka tanthauzo ndi phindu lenileni la mfundo zimene mwasankhazo.
Nkhani Yolangiza
Imeneyi ingazikidwe pa nkhani yofalitsidwa kale, monga ya mu Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! kapena buku lina. Kaŵirikaŵiri, nkhaniyo imakhala ndi mfundo zambiri zosati n’kuzitha m’nthaŵi yoperekedwa. Kodi muyenera kuikamba motani nkhaniyo? Ikambeni ngati mphunzitsi, osati ngati munthu wongofotokoza nkhani chisawawa ayi. Woyang’anira ayenera kukhala “wokhoza kuphunzitsa.”—1 Tim. 3:2.
Yambani kukonzekera mwa kuŵerenga nkhaniyo. Ŵerengani malemba ake. Sinkhasinkhani. Yesetsani kuchita zimenezo nthaŵi ikalipo lisanafike tsiku la nkhani yanu. Kumbukirani kuti abale amalimbikitsidwanso kuŵerengeratu magwero a nkhani yanuyo. Choncho, udindo wanu si kungoibwereza nkhaniyo ayi, kapena kungopereka chidule chake, koma kuonetsa mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake. Fotokozani mfundo zoyenera za nkhaniyo m’njira imene ingapindulitsedi mpingo.
Mmene mwana aliyense amakhalira ndi khalidwe lakelake, mpingo uliwonse umakhalanso ndi makhalidwe amene umadziŵika nawo. Kholo lodziŵa kuphunzitsa silimangobwereza kwa mwana wake mfundo za makhalidwe abwino zoloŵeza pamtima. Limakambirana ndi mwanayo. Limalingalira za khalidwe la mwanayo ndi mavuto amene mwanayo akukumana nawo. Mofananamo, aphunzitsi mumpingo amayesetsa kuzindikira zosoŵa za anthu amene akulankhula nawo ndipo amaperekapo thandizo. Komabe, mphunzitsi wozindikira amapeŵa kupereka zitsanzo zimene zingachititse manyazi wina mwa omverawo. Iye amatchula mapindu omwe amakhalapo poyenda m’njira ya Yehova ndipo amaunika uphungu wa m’Malemba umene ungathandize mpingo kuthana ndi mavuto amene ukukumana nawo.
Kuphunzitsa kwabwino kumakhudza mitima ya omvera. Kuphunzitsa koteroko sikutheka mwa kungotchula mfundo zakutizakuti, koma kuphunzitsa omverawo kuzindikira cholinga cha mfundozo. Kumafunanso kukhala ndi chidwi chenicheni pa awo amene akuphunzitsidwa. Abusa auzimu ayenera kudziŵa nkhosa zawo. Ngati mwachikondi amakumbukira mavuto amene anthu osiyanasiyana amakumana nawo, adzakhoza kulankhula mowalimbikitsa, akumasonyeza kuti amamvetsa mkhalidwe wawo, amawamvera chifundo, ndipo amawaganizira.
Monga momwe aphunzitsi aluso amadziŵira, nkhani iyenera kukhala ndi cholinga chomveketsedwa bwino lomwe. Nkhani iyenera kukambidwa m’njira younika bwino mfundo zazikulu kuti zikakumbukike. Omverawo ayenera kumakumbukira malingaliro othandiza amene adzakhudza miyoyo yawo.
Msonkhano wa Utumiki
Pokamba nkhani yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu, udindo wanu ungakhale wosiyanako. Apa, si kwa inu kwenikweni kusankha mfundo zoyenerera. Kwanu n’kufotokozera mokwanira omvera anu zimene zalembedwa kale. Thandizani omvera kulingalira pa malemba amene ali maziko a uphungu uliwonse umene waperekedwa. (Tito 1:9) Nthaŵi imakhala yochepa, moti kaŵirikaŵiri siidzakulolani kuwonjezerapo mfundo zina.
Komanso, nthaŵi zina mungapemphedwe kukamba nkhani yosachokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nkhaniyo ingachokere mu Nsanja ya Olonda, kapena angangokupatsani mfundo zina pang’ono. Monga mphunzitsi, ndi udindo wanu kulingalira zosoŵa za mpingo mogwirizana ndi nkhani imene mwapatsidwayo. Mungafune kugwiritsa ntchito chitsanzo chachidule koma cholunjika pa mfundo, kapena mungasimbe chochitika choyenerera. Kumbukirani kuti udindo wanu si kungofotokoza mfundo za nkhaniyo, koma kukamba nkhaniyo m’njira imene idzathandiza mpingowo kugwira ntchito imene yaperekedwa m’Mawu a Mulungu ndi kuti azikondwa poigwira.—Mac. 20:20, 21.
Pamene mukukonzekera nkhani yanu, ganizirani mikhalidwe ya anthu a mumpingo wanu. Ayamikireni pa zimene amachita. Kodi angakulitse motani luso lawo ndi chisangalalo chawo mu ulaliki ngati agwiritsa ntchito malingaliro operekedwa m’nkhaniyo?
Kodi nkhani yanu ili ndi chitsanzo kapena mbali yokhala ndi anthu oti muwafunse mafunso? Ngati zili choncho, ziyenera kukonzedwa bwino nthaŵi ikalipo. Mungafune kupempha munthu wina kuti akonze mbali zimenezo, koma kachitidweko kaŵirikaŵiri sikakhala ndi mapindu abwino kwenikweni. Ngati n’kotheka, inu eni akenu yesezani chitsanzocho kapena mbali yofunsa anthuyo tsiku la msonkhanowo lisanafike. Onetsetsani kuti mbali imeneyi ya nkhani yanu ikayendetsedwa m’njira yomveketsa bwino malangizo omwe akaperekedwe.
Misonkhano Ikuluikulu
Abale amene amakula m’makhalidwe abwino auzimu, amenenso amalankhula ndi kuphunzitsa mwaluso pamaso pa anthu, m’kupita kwa nthaŵi angapemphedwe kutenga mbali m’pulogalamu ya misonkhano ngati wadera kapena wachigawo. Misonkhano imeneyi ili zochitika zapadera za maphunziro auzimu. Gawo limenelo lingakhale nkhani yoŵerenga, autilaini, malangizo a seŵero la m’Baibulo ndi mmene lingatithandizire masiku ano, kapena ndime ya malangizo. Ngati mwapatsidwa mwayi wokhala m’pulogalamu imeneyo, ŵerengani nkhani imene mwapatsidwayo mosamala kwambiri. Iphunzireni kufikira mutazindikira phindu lake.
Aja amene amapatsidwa nkhani yoŵerenga, ayenera kuŵerenga mawu onse a nkhaniyo mmene awalembera. Saloledwa kusintha mawu kapena kusuntha mfundo zake m’njira iliyonse. Amaiphunzira kotero kuti azindikire bwino lomwe mfundo zake zazikulu ndi mmene azifotokozera. Amayeseza kuŵerenga mokweza mpaka atakhoza kukamba nkhaniyo motsindika bwino ganizo, mosangalala, mwachikondi, mwa mzimu wake, moona mtima, ndi mwachidaliro, komanso ndi mphamvu ya mawu yoyenerera pagulu lalikulu la omvera.
Abale amene amapatsidwa nkhani ya autilaini ayenera kufotokoza mfundo zawo motsatira autilainiyo. M’malo mongoŵerenga pa autilaini pokamba nkhaniyo, kapena kuilemba yonse ngati nkhani yoŵerenga, wokambayo ayenera kuikamba mochokera mu mtima. M’pofunika kusunga nthaŵi zosonyezedwa pa autilaini kotero kuti aunike bwino mfundo zazikulu. Wokamba nkhani ayenera kumagwiritsa ntchito bwino malingaliro ndi malemba operekedwa pansi pa mfundo zazikuluzo. Sayenera kuloŵetsapo mfundo zowonjezera zimene angazikonde ndi kusiya mfundo zoperekedwa pa autilainiyo. Ndi iko komwe, Mawu a Mulungu ndiwo maziko a malangizowo. Ntchito ya akulu achikristu yangokhala ‘kulalikira mawu.’ (2 Tim. 4:1, 2) Choncho, wokamba nkhani ayenera kusamala kwambiri malemba a pa autilainiyo—awafotokoze ndi kuonetsa mmene amagwirira ntchito.
Musakhale Wozengereza
Kodi mumpingo wakwanu mumakhala ndi mwayi wokamba nkhani pafupipafupi? Kodi mungatani kuti muzikonzekera bwino nkhani zonsezo ndi kuzikamba mogwira mtima? Peŵani kukonzekera nkhani zanu mochedwa.
Nkhani zimene zimapindulitsadi mpingo zimafuna kusinkhasinkha mozama pasadakhale. Choncho, khalani ndi chizoloŵezi chomaŵerenga nkhani iliyonse mutangoilandira. Izi zidzakuthandizani kuisinkhasinkha pamene mukuchita zinthu zina. M’kati mwa masiku angapo kapena milungu ingapo musanakambe nkhani yanu, mungamve ndemanga zimene zingakuthandizeni kuona mmene mungafotokozere bwino kwambiri mfundo zanu. Mungakumane ndi mikhalidwe yokhudzana ndendende ndi nkhani yanu. Kuŵerenga ndi kulingalira pa nkhani yanu pamene mwailandira kuyenera kutenga nthaŵi, koma ndi nthaŵi yophula kanthu imeneyo. Potsirizira pake pamene mukhala pansi tsopano kuti muiyale autilaini yanu, mudzatuta mapindu a kuilingalira bwino nkhaniyo, kumene munakuchita nthaŵi ikalipo. Kukonzekera nkhani mwa njira imeneyi kumachepetsa nkhaŵa ndipo kudzakuthandizani kukamba nkhani m’njira yothandiza imene imafika pamtima mpingo wonse.
Ngati muyamikira ndi mtima wonse mphatso imene yaikizidwa kwa inu yokhudzana ndi mapulogalamu amene Yehova amaphunzitsira anthu ake, mudzakhala mukum’lemekeza kwambiri ndipo mudzakhala dalitso kwa okondeka a Yehova.—Yes. 54:13; Aroma 12:6-8.