Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/08 tsamba 2-3
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 11/08 tsamba 2-3

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati anthu anena kuti ali ndi ana, agawireni buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. January 2009: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

◼ Tikulimbikitsa ofalitsa onse amene sanalembebe khadi la chikalata chosasinthika chopatsa munthu mphamvu yondisankhira thandizo la mankhwala (DPA) kuti alembe. Khadi la DPA limateteza ufulu wanu wokana kuikidwa magazi. Ngati munthu angafunikire thandizo, akulu angamuthandize.—Onani mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006.

◼ Kuyambira January 1, 2009, tidzasiya kugwiritsa ntchito dzina lakuti “woyang’anira wotsogolera.” M’malo mwake, tizigwiritsa ntchito dzina lakuti “wotsogolera bungwe la akulu.”

◼ Nthawi zambiri, zilengezo zofunika kwambiri zimaperekedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu zokhudza kayendetsedwe ndi kufunsira mabuku. Atumiki a mabuku amayenera kuwerenga zilengezo zimenezo akangolandira Utumiki Wathu wa Ufumu kuti achite mwamsanga zimene akuuzidwazo.

◼ Tikukumbutsa ofalitsa kuti mabuku a zilembo za akhungu ndi okwera mtengo ndipo amafuna ndalama zambiri kuti apangidwe. Ndi udindo wathu kupereka zopereka za mabuku amenewa. Mlembi wa mpingo akamavomereza Fomu Yofunsira Mabuku (S-14), afunika kutsimikizira kuti mabukuwo ndi a ofalitsa kapena maphunziro a Baibulo amene akuchita bwino. Ayenera kusonyeza bwinobwino pa S-14 kuti wapenda mosamala zinthu zimene zapemphedwazo ndipo wavomereza. Amene amalandira Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! ya zilembo za akhungu ayeneranso kuganizira za mtengo wake.

◼ Chidziwitso kwa Atumiki a Magazini: Ena afunsapo kuti angatumize liti fomu yofunsira magazini owonjezera a ntchito yapadera ya mwezi wa March, April ndi May 2009. Mfundo yake ndi yomwe ija yakuti mafomu ofunsira magaziniwa ayenera kutumizidwa kutatsala miyezi yosachepera itatu lisanafike deti la magaziniyo. Mwachitsanzo, ngati mukufunsira magazini a mwezi wa March, muyenera kutumiza fomuyo pasanafike pa December 8. Ngati ndi a April, pasanafike pa January 5 ndipo ngati ndi a May, tumizani pasanafike pa February 9. Ngati fomu yofunsira yafika mochedwa, tingadzaisinthe kuti ikhale ya magazini a m’tsogolo. Zili choncho chifukwa chakuti panthawi imene fomu yochedwayo yafika, magaziniwo angakhale atatha. Tikufuna kupewa kulandira mafomu ochedwa amene akufunsira zinthu zofunika mwamsanga. Chotero, muzitumiza mafomu anu mofulumira.

◼ Mipingo iyambe kuitanitsa Watchtower Library—2008 (cdly08). Imeneyi ndi yofunsira mwapadera, ndipo inakonzedwera ofalitsa obatizidwa ndi osabatizidwa ndipo mungaiitanitse kudzera kumpingo basi. Si yogawira m’munda komanso si yopatsa anthu amene amangochita chidwi ndi Mboni za Yehova. Ofalitsa amene amagwiritsa ntchito kwambiri Watchtower Library ndipo sagwiritsanso ntchito mabaundi voliyumu, angachite bwino kuganizira ngati angafunikebe kumaitanitsa mabaundi voliyumuwo. Watchtower Library—2008 idzakhala ya Chifrenchi, Chingelezi ndi Chipwitikizi.

◼ Ma CD Atsopano Omwe Alipo:

Live With Jehovah’s Day in Mind (cdjd)—Chifrenchi

◼ Ma DVD Atsopano Omwe Alipo:

Album for The Watchtower Announcing Jehovah’s Kingdom 2009 (dvcw09)—Chinenero Chamanja cha ku America

Learn From the Great Teacher (dvlr)—Chinenero Chamanja cha ku America

Organized to Share Good News and Whole Association of Brothers (dvjwa)—Chinenero Chamanja cha ku America

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena