Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira November 10
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Phatikizanipo ndemanga za woyang’anira utumiki za zimene mpingo wachita pofola gawo lawo ndi kugawira kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Popeza ofalitsa ambiri ayamba kale kugawira Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya November, pemphani omvera kuti afotokoze mmene agawirira magaziniwo ndiponso zotsatira zabwino zimene apeza.
Mph.15: Musasiye Kukhala ndi Mzimu Wachikondi ndi Wopatsa. Nkhani yokambidwa ndi mkulu, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2008, tsamba 6 ndi 7.
Mph.20: “Tili ndi Chuma Chamtengo Wapatali Chofunika Kugawira Ena.”a Pokambirana ndime 2, apempheni omvera kuti afotokoze mfundo za m’Baibulo zimene zinawagwira mtima kuti abwere m’gulu la Yehova, kapena zimene azimvetsa kwambiri ndi kuzikonda kuchokera panthawi imene anabatizidwa.
Mlungu Woyambira November 17
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.15: Bokosi la Mafunso.*
Mph.20: “N’zotheka Inuyo Kukhala Mphunzitsi.”b Funsani wofalitsa kapena mpainiya amene anathetsa maganizo odzikayikira akuti sangakwanitse kuchititsa phunziro la Baibulo. Kodi iye anachita chiyani podalira Yehova kuti amuthandize? Kodi gulu lamuthandiza m’njira zotani kuti akhale woyenerera? Kodi wapeza madalitso otani chifukwa chochititsa maphunziro a Baibulo?
Mlungu Woyambira November 24
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka, olembedwa pa sitetimenti. Tchulani mabuku ogawira mu December, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri.
Mph.20: Zosowa za pampingo.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili m’magaziniwa, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene zingasangalatse anthu a m’gawo lanu. Kodi ndi mafunso otani ndipo ndi malemba ati amene angagwiritse ntchito posonyeza nkhani za m’magaziniwo? Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito ulaliki wa mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Komanso mkulu achite chitsanzo chachidule chimene iye wakonzekera mogwirizana ndi nkhani ya m’magaziniwo imene anthu a m’gawo lanu angachite nayo chidwi.
Mlungu Woyambira December 1
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa November.
Mph.15: Zokumana nazo. Dziwitsani mpingo kuti gawo lanu mwalifola kufika pati pogawira kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Pemphani omvera kuti afotokoze zimene zinachitika pogawira kapepalako kapena pokagwiritsa ntchito kuti ayambitse phunziro la Baibulo. Komanso apempheni kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo mu November pogawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Sankhani chokumana nacho chimodzi kapena ziwiri zabwino ndi kuchitira chitsanzo.
Mph.20: “Akonzekeretseni Atsopano Kupirira Chitsutso.”c Pokambirana ndime 2, kambiranani mwachidule mmene mfundo za m’buku la Kukambitsirana, pamutu wakuti “Mboni za Yehova,” zingathandizire ophunzira Baibulo kuyankha mafunso ochokera kwa achibale ndi mabwenzi awo.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.