Akonzekeretseni Atsopano Kupirira Chitsutso
1 Anthu akayamba kuphunzira Baibulo ndi ‘kufuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu,’ Satana amawalondalonda kuti aziwatsutsa. (2 Tim. 3:12) Iwo angatsutsidwe ndi anzawo akuntchito, akusukulu, kapena anthu oyandikana nawo. Nthawi zambiri zimakhala zovuta ngati amene akutsutsa atsopanowo ndi achibale awo, amene pochita zimenezo, amaona ngati akufuna kuwathandiza.—Mat. 10:21; Maliko 3:21.
2 Ananeneratu Kuti Tidzatsutsidwa: Atsopano ayenera kudziwa kuti adzazunzidwa, ndipo zimenezi zimasonyeza kuti iwo tsopano ndi ophunzira enieni a Khristu. (Yoh. 15:20) Nthawi zina, anthu angawatsutse chifukwa cha maganizo olakwika amene anthuwo amakhala nawo ponena za Mboni za Yehova. Musaiwale kuti munthu akamachitiridwa chipongwe chifukwa chokhala wotsatira Yesu ndiponso kumvera Mulungu, amakhala wosangalala kwambiri. (Mac. 5:27-29, 40, 41) Atsimikizireni atsopanowo kuti, Yehova amawakonda ndipo adzawathandiza. (Sal. 27:10; Maliko 10:29, 30) Choncho, ngati iwo apitirizabe kusunga umphumphu wawo, amakhala kumbali ya Yehova pankhani ya ulamuliro wa m’chilengedwe chonse.—Miy. 27:11.
3 Ubwino Wodziwa Zinthu Molondola: Athandizeni ophunzira Baibulo kuona kuti afunika kusasiya kuphunzira kuti adziwe zinthu molondola, ngakhale angakumane ndi mavuto otani. Satana amagwiritsa ntchito chitsutso pofuna kuletsa zimene iwo akuphunzira kuti zisazike mizu m’mitima yawo yophiphiritsa. (Miy. 4:23; Luka 8:13) Afunika kusasiya kuphunzira kuti adziwe molondola Mawu a Mulungu, chifukwa zimenezi zidzawathandiza kukhala okhazikika m’chikhulupiriro.—Sal. 1:2, 3; Akol. 2:6, 7.
4 Kupirira N’kofunika: Panthawi ya mavuto, kupirira n’kofunika kwambiri ndipo kungabale zipatso zabwino. (Luka 21:16-19) Atsopano akamapirira chitsutso, amapindula ndiponso amapindulitsa ena. Iwo amaona mphamvu ya Yehova polandira madalitso ochuluka amene iye amapereka kwa anthu omwe amapirira mokhulupirika.—Yak. 1:12.
5 Mtumwi Paulo anasangalala kwambiri ataona mmene abale a ku Tesalonika anapitira patsogolo mwauzimu. Anathokoza Mulungu chifukwa cha iwo, popeza iyeyo anali atathandiza ambiri a iwo kuphunzira choonadi. (2 Ates. 1:3-5) Ifenso, tingasangalale ngati tikonzekeretsa ophunzira Baibulo kuti azipirira chitsutso.