Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/08 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira December 8
  • Mlungu Woyambira December 15
  • Mlungu Woyambira December 22
  • Mlungu Woyambira December 29
  • Mlungu Woyambira January 5
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 12/08 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira December 8

Nyimbo Na. 19

Mph 10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo za pa tsamba 4 bwerezani mwachidule zomwe tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December. Pemphani omvera amene agawirapo magaziniwa kuti afotokoze zimene anachita. Anene nkhani, funso komanso lemba limene anagwiritsa ntchito.

Mph 15: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2009. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Kumbutsani omvera mfundo zofunika kwanuko za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2008. Fotokozaninso ntchito ya mlangizi wothandiza. Alimbikitseni onse kuchita khama kuti akambe nkhani zimene apatsidwa, kupereka ndemanga pa mfundo zazikulu za m’Baibulo komanso kutsatira malangizo amene apatsidwa kuchokera m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

Mph 20: “Kodi Mukugwiritsa Ntchito Buku la Kukambitsirana?”a Pokambirana ndime 4, pemphani mpainiya kapena wofalitsa wina waluso kuti achite chitsanzo cha mmene tingagwiritsire ntchito buku la Kukambitsirana poyankha funso lakuti, ‘N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova sizimakondwerera Khirisimasi?’

Nyimbo Na. 6

Mlungu Woyambira December 15

Nyimbo Na. 178

Mph 10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph 10: Bwerezani Mfundo Muutumiki. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 207. Pangani chitsanzo chosonyeza mmene mungabwerezere mfundo muutumiki pogwiritsa ntchito njira imodzi kapena ziwiri zimene zafotokozedwa pa tsamba 207.

Mph 25: Kukhala Atumiki Opita Patsogolo ndi Otha Kusintha. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2005, masamba 28 mpaka 29, ndime 6 mpaka 14. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki kapena mkulu wina. Fotokozani mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi mogwirizana ndi gawo lanu.

Nyimbo Na. 157

Mlungu Woyambira December 22

Nyimbo Na. 75

Mph 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Tchulani mabuku ogawira mu January, ndipo mkulu achite chitsanzo cha mmene tingagawire.

Mph 15: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January. Nkhani yokambirana ndi omvera. Fotokozani mwachidule mfundo za m’magaziniwa ndipo funsani omvera kuti atchule nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lanu ndipo anene chifukwa chake. Pemphani omvera kuti atchule zimene anganene poyamba kukambirana ndi munthu. Kodi ndi mafunso komanso malemba ati amene angagwiritsidwe ntchito asanagawire magazini? Malizani nkhaniyi ndi chitsanzo cha mmene tingagawire magazini iliyonse pogwiritsa ntchito mfundo za pa tsamba 4 kapena mfundo zimene mukuona kuti zingasangalatse anthu a m’gawo lanu.

Mph 20: “Tsiku Lapadera Loyambitsa Maphunziro a Baibulo.”b Lengezani mlungu umene mpingo wanu udzayambitse maphunziro a Baibulo mu January. Kambiranani njira zoyambitsira maphunziro zimene zasonyezedwa m’zofalitsa zimene zili m’ndime 3 ndipo chitani chitsanzo cha njira imodzi kapena ziwiri.

Nyimbo Na. 133

Mlungu Woyambira December 29

Nyimbo Na. 60

Phunziro la Baibulo la Mpingo:

cl tsa. 114 ndime 15 mpaka tsa. 117 ndi bokosi

Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:

Kuwerenga Baibulo: Chivumbulutso 15-22

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Msonkhano wa Utumiki:

Nyimbo Na. 153

Mph 5: Zilengezo za pampingo.

Mph 10: Zosowa za pampingo.

Mph 20: “Kulalikira Kumafuna Kupirira.”c Ngati nthawi ilipo pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.

Nyimbo Na. 155

Mlungu Woyambira January 5

Nyimbo Na. 35

Phunziro la Baibulo la Mpingo:

cl tsa. 118 mpaka 123 kulekeza pa kamutu

Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:

Kuwerenga Baibulo: Genesis 1-5

Na. 1: Genesis 3:1-15

Na. 2: Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso (lr-CN mutu 1)

Na. 3: Kodi Ndi Ntchito Yotani Yomwe Sipita Pachabe? (1 Akor. 15:58)

Msonkhano wa Utumiki:

Nyimbo Na. 98

Mph 5: Zilengezo za pampingo.

Mph 10: Tsatirani Yesu Pankhani Yokonda Anthu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002, masamba 18 mpaka 20, ndime 13 mpaka 22.

Mph 20: Sonyezani ‘Chipatso cha Mzimu.’ Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 2001, masamba 15 mpaka 17. Tsindikani ubwino wa kusonyeza chipatso cha mzimu nthawi zonse.—Agal. 5:22, 23.

Nyimbo Na. 114

[Mawu a M’munsi]

a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena