Ndandanda ya Mlungu wa April 20
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 20
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 18 ndime 1-6
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Eksodo 15-18
Na. 1: Eksodo 15:1-19
Na. 2: Kodi Kupewa Kulambira Konyenga Kumatanthauza Chiyani?
Na. 3: Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima (lr-CN mutu 15)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.15: Konzekerani kugawira magazini ya Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May. Funsani omvera kuti atchule nkhani zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawo lanu ndipo anene chifukwa chake. Chitani chitsanzo cha mmene mungagawire magazini iliyonse. Mu chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene mungayambitsire phunziro pa ulendo wobwereza.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2007, tsamba 3.
Mph.15: “Phunzitsani Anthu Amene Amavutika Kuwerenga.” Pokambirana ndime 3, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mpainiya akugwiritsa ntchito bwino chithunzi chimene chili m’buku limene akuphunzitsira.