Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi aonetseni ndi kukambirana nawo kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?
◼ Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya chaka chonse sidziikidwanso mu Utumiki Wathu wa Ufumu. M’malo mwake, mpingo uliwonse uzilandira ndandanda ziwiri, imodzi izikhomedwa pabolodi la chidziwitso mu Nyumba ya Ufumu ndipo inayo izipatsidwa kwa woyang’anira sukulu kuti azigwiritsa ntchito pogawira nkhani za m’sukulu. Wofalitsa aliyense azilandirabe Utumiki Wathu wa Ufumu mwezi uliwonse, ndipo uzikhala ndi ndandanda ya Phunziro la Baibulo la Mpingo, Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndiponso Msonkhano wa Utumiki wa mlungu uliwonse.
◼ Kuyambira mlungu wa January 4, 2010, buku la “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu” lizidzaphunziridwa pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Mipingo imene ikufuna buku limeneli iyenera kuitanitsa pa oda ya mabuku yotsatira.