Ndandanda ya Mlungu wa November 2
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 2
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 28, ndime 14 mpaka 21, ndi bokosi patsamba 289
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 14-18
Na. 1: Deuteronomo 15:1-15
Na. 2: Kodi Kuopa Mulungu Kumaphatikizapo Chiyani?
Na. 3: Mulungu Anakumbukira Mwana Wake (lr-CN mutu 39)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Kukambirana ndi omvera. Sankhani ofalitsa angapo ndipo apempheni kuti afotokoze zimene zinachitika pamene amayambitsa maphunziro pa tsiku limene linasankhidwa kuchita ntchito yapadera imeneyi. Lengezani tsiku lotsatira limene lasankhidwa kudzayambitsa maphunziro a Baibulo, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingayambitsire maphunziro a Baibulo.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kulalikira M’kalata. Nkhani yokambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 71 mpaka tsamba 73.