Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/09 tsamba 3
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 10/09 tsamba 3

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 26, 2009.

1. Popeza Yehova anauza Balamu kuti atsagane ndi anthu a Balaki, n’chifukwa chiyani Yehova anakwiya Balamuyo atatsagana nawo? (Num. 22:20-22) [w04-CN 8/1 tsa. 27 ndime 2]

2. Kodi “nsanje” imene Pinehasi anasonyeza posafuna kuti wina azipikisana ndi Yehova, ingatithandize bwanji kuganizira bwino kudzipereka kwathu kwa Mulungu? (Num. 25:11) [w95-CN 3/1 tsa. 16 ndime 13]

3. N’chifukwa chiyani Yoswa anasankhidwa kuti alowe m’malo mwa Mose? (Num. 27:15-19) [w02-CN 12/1 tsa. 12 ndime 1]

4. Kodi lemba la Numeri 31:27 ndi lolimbikitsa motani kwa Akhristu masiku ano? [w05-CN 3/15 tsa. 24]

5. Kodi kukhala ndi midzi yopulumukirapo kunawathandiza bwanji anthu mu Isiraeli? (Num. 35:11, 12) [w95-CN 11/15 tsa. 14 ndime 17]

6. N’chifukwa chiyani kuzindikira kuli kofunika kwa Akhristu, nanga kodi munthu wozindikira amatani? (Deut. 1:13) [w03-CN 1/15 tsa. 30; w00-CN 10/1 tsa. 32 ndime 1-3]

7. Kodi Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwanji chilungamo cha Mulungu? (Deut. 4:8) [w02-CN 6/1 tsa. 14 ndime 8–tsa. 15 ndime 9-10]

8. Malinga ndi lemba la Deuteronomo 6:16-18, kodi njira yoyenera yoyesera Yehova ndi iti, nanga yolakwika ndi iti? [w04-CN 9/15 tsa. 26 ndime 6]

9. Kodi mawu otuluka m’kamwa mwa Yehova anakwaniritsa bwanji zosowa za Aisiraeli, nanga angakwaniritse bwanji zosowa zathu masiku ano? (Deut. 8:3) [w99-CN 8/15 tsa. 25-26]

10. Kodi lemba la Deuteronomo 12:16, 24 limatithandiza bwanji kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chithandizo chakuchipatala chogwiritsa ntchito magazi athu omwe? [w00-CN 10/15 tsa. 30 ndime  7]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena