Ndandanda ya Mlungu wa December 21
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 21
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 31 ndime 6-12
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 9-11
Na. 1: Yoswa 9:1-15
Na. 2: Zimene Zikutidziwitsa Kuti Armagedo Ili Pafupi (lr-CN mutu 47)
Na. 3: Mungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu Lamtendere (lr-CN mutu 48)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza woyang’anira kagulu ka utumiki wakumunda akukambirana ndi wofalitsa wachinyamata nkhani imene wakonzekera komanso chifukwa chake wasankha kukakambirana ndi anthu nkhani imeneyo. Atchulenso funso ndiponso malemba amene akagwiritse ntchito. Wachinyamatayo afotokoze kuti iye anaganizira nkhani inayake m’magaziniyo koma akufuna kuti athandizidwe mmene angakaifotokozere. Pogwiritsa ntchito nkhani imene akuiganizirayo, athandizane kukonza funso komanso kusankha malemba amene akagwiritse ntchito.
Mph. 15: “‘Perekani Moyo Wanu’ kwa Ophunzira Anu.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 2, funsani wofalitsa mmodzi kuti afotokoze zinthu zingapo zimene amachita posonyeza kuti amakonda ophunzira ake. Kodi zotsatira zake zakhala zotani? Funsaninso wofalitsa wina kuti afotokoze mmene anapindulira ndi chikondi chimene munthu amene ankamuphunzitsa Baibulo ankamusonyeza.