Ndandanda ya Mlungu wa December 28
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 28
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 31 ndime 13-23, ndi bokosi patsamba 319
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 12-15
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Fotokozani nkhani yakuti “Kodi Mwakonzekera Kuimbira Yehova Pamisonkhano?” Alimbikitseni onse kuti azibwera ndi buku lawo latsopano la nyimbo kumisonkhano kuyambira mwezi wa January, ngati ali nalo.
Mph. 10: Kambiranani ndi omvera za zinthu zimene anthu a m’gawo lanu amakonda kunena akafuna kuti tisawalalikire. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito mfundo imodzi ya mu nkhaniyi. (Onani tsamba 58 mpaka 62 m’buku la Kukambitsirana.)
Mph. 10: Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Lengezani tsiku lotsatira loyambitsa maphunziro a Baibulo. Kambiranani ndi omvera mmene ntchito yoyambitsa maphunziro a Baibulo yathandizira mpingo wanu? Pemphani mpainiya kapena wofalitsa aliyense kuti afotokoze kapena achite chitsanzo chosonyeza ulaliki umene wakhala wogwira mtima kwambiri m’gawo lanu.
Mph. 10: Mabuku ogawira mu January. Fotokozani mwachidule zimene zili m’mabukuwo. Kambiranani ndi wofalitsa njira zimene zingagwiritsidwe ntchito poyambitsa phunziro la Baibulo mwamwayi pogawira mabukuwo. Limbikitsani aliyense kuti akhale ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo mwezi uno.