‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
1. M’miyezi ikubwerayi, kodi Phunziro la Baibulo la Mpingo lidzatipatsa mwayi wotani?
1 Nkhani zinayi za Mauthenga Abwino zimafotokoza zambiri za moyo wa padziko lapansi wa Yesu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu. Popeza kuti Akhristu ayenera ‘kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri,’ tifunika kumadzakonzekera bwino komanso kumvetsera mwatcheru tikadzayamba kuphunzira buku lakuti ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’ pa Phunziro la Baibulo la Mpingo kuyambira mlungu wa January 10, 2011. (1 Pet. 2:21; Maliko 10:21) Tidzafunika kuchita chidwi kwambiri ndi mbali za moyo wa Yesu zimene zingatilimbikitse mu utumiki wathu.
2. Kodi chitsanzo cha Yesu cha kupirira chikutiphunzitsa chiyani?
2 Chitsanzo Chimene Yesu Anatisiyira: Kodi munayamba mwatsutsidwapo mukulalikira khomo ndi khomo? Tikakumana ndi zinthu zoterezi timatsimikizira mawu a Yesu akuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yoh. 15:20) N’zoona kuti sitinganene kuti nthawi zonse pamene tatsutsidwa ndiye kuti tazunzidwa. Ngakhale kuti Yesu ankazunzidwa, chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake chinamuthandiza kupirira mayesero onse amene anakumana nawo. Nafenso tikhoza kuika maganizo athu onse pa kuchita zinthu zimene zimasangalatsa Yehova ndiponso pa mphoto imene tidzapeze tikakhala okhulupirika. Zimenezi zidzatithandiza kuti ‘tisatope ndiponso kuti tisalefuke.’ (Aheb. 12:2, 3; Miy. 27:11) Tikamapitirizabe utumiki wathu, tingakhale otsimikiza kuti Khristu Yesu adzatithandiza.—Mat. 28:20.
3. Kodi tingatsanzire bwanji mmene Yesu ankaonera utumiki?
3 “Ndi Zimene Anandituma Kudzachita”: Yesu ankaona kuti ntchito yolalikira za Ufumu inali yofunika kwambiri pa moyo wake. (Luka 4:43) Anali wodzipereka kwambiri pa utumiki. Ankaona kuti ntchitoyi ndi yofunika kuigwira mwachangu, moti nthawi zonse ankayesetsa kupeza mipata yoti alankhule za Ufumu. Popeza ndife otsatira a Yesu, kodi tiyenera kuchita zotani potengera chitsanzo chake? Kodi pali anthu ena amene tingawalalikire uthenga wabwino pamene tikugwira ntchito zathu za tsiku ndi tsiku? Chikondi chimene Khristu ali nacho chitikakamize kulengeza uthenga wabwino kwa anthu ambiri mmene tingathere.—2 Akor. 5:14.
4. Kodi tingawonjezere bwanji luso lathu la mu utumiki?
4 “Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyu N’kale Lonse”: Anthu amene ankamvetsera Yesu ankagoma ndi kaphunzitsidwe kake. (Yoh. 7:46; Mat. 7:28, 29) Kodi ankasiyana bwanji ndi aphunzitsi ena? Yesu ankakonda choonadi chimene ankaphunzitsa, ankakonda anthu amene ankawalalikira, komanso ankagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana pophunzitsa. Kutsanzira Mphunzitsi Wamkulu kungatithandize kuwonjezera luso lathu la mu utumiki.—Luka 6:40.
5. Kodi tikhale ndi cholinga chotani pamene tikuphunzira buku lakuti ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’?
5 Izi ndi zochepa chabe mwa zinthu zapadera zimene timaphunzira pa moyo wa Yesu. Kodi moyo wa Yesu ungatiphunzitse zinthu zina ziti? Pamene mukuphunzira za moyo wa Yesu pa Phunziro la Baibulo la Mpingo, khalani ndi cholinga choti “mudziwe chikondi cha Khristu” potsanzira zimene ankalankhula komanso kuchita.—Aef. 3:19.