Uzilemekeza Yehova ndi Zinthu Zako Zamtengo Wapatali—Gawo 2
1. Kodi bokosi lachiwiri limatchulidwa kuti chiyani?
1 M’gawo loyamba lomwe linali ndi mutu wakuti “Lemekeza Yehova ndi Chuma Chako,” tinakambirana za bokosi la Ntchito ya Padziko Lonse. (Mateyu 24:14) M’gawo lachiwiri lino tikambirana za bokosi lachiwiri lakuti “Zopereka Zothandiza Mpingo Wathu.” Kodi bokosi limeneli tiyenera kuligwiritsa ntchito bwanji?
2. Kodi bokosi limeneli limagwiritsidwa ntchito motani?
2 Zopereka Zothandiza Mpingo Wathu: Timagwiritsa ntchito bokosi la “Zopereka Zothandiza Mpingo Wathu” pochirikizira mpingo wathu. Monga mukudziwira, mpingo umafunika kulipirira zinthu za pa Nyumba ya Ufumu zimene zawonongeka, kusamalira woyang’anira dera akamayendera mpingowo, komanso kuchirikizira akaunti ya dera ngati pakufunika kutero. Komanso m’madera ena mipingo imafunika kulipira zinthu ngati madzi ndi magetsi. Werengani 2 Mbiri 34:8-11.
3. Fotokozani mmene tingasonyezere kuti timayamikira mwayi wogwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu yathu.
3 Kuwonjezera apo, tingagwiritsirenso ntchito bokosi limeneli pamene tikufuna kupereka ndalama ku Sosaite chifukwa chogwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu. M’zaka zaposachedwapa, ku Malawi kuno kwamangidwa Nyumba za Ufumu zochuluka ndipo ntchito imeneyi yadya ndalama zambiri. Kodi sitimayamikira mmene Yehova amatisamalirira mwauzimu kudzera m’gulu lake? Pofuna kusonyeza kuyamikira kuti tili ndi mwayi wokhala ndi Nyumba ya Ufumu yathuyathu tingaponye zopereka m’bokosi limeneli. Ndipo chaka chilichonse mwezi wa May, mpingo uyenera kuonanso ndalama zimene ukhoza kumapereka posonyeza kuyamikira kuti uli ndi Nyumba ya Ufumu yawoyawo. Wofalitsa aliyense adzapemphedwa kulemba pakapepala ndalama zimene angathe kumapereka mwezi ndi mwezi. Zimenezi ziyenera kuchitika motsogoleredwa ndi bungwe la akulu. Ndalama zimene mungagwirizane ziyenera kukhala zoti mpingowo ungakwanitsedi kumapereka mwezi ndi mwezi. Wofalitsa aliyense ayenera kuyesetsa kupereka ndalama zimene analonjeza kuti azipereka mwezi uliwonse, mogwirizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wake.—1 Akor. 16:1, 2; 2 Akor. 9:7.
4. Kodi cholinga cha Makonzedwe Othandiza pa Nyumba za Ufumu n’chotani?
4 Kuwonjezera pa zimene tafotokoza pamwambazi, timatumiza ndalama ku Sosaite kamodzi pa chaka zotetezera Nyumba ya Ufumu (Inshuwalansi) ngati itawonongedwa ndi akuba kapena masoka a chilengedwe, monga kusefukira kwa madzi. Zimenezi zimatchedwa kuti Makonzedwe Othandiza pa Nyumba za Ufumu (KHAA). Mpingo ndi umene uyenera kulipira ndalama zimenezi. Choncho, ndalamazi ziyenera kuchotsedwa pa ndalama zimene mpingo uli nazo.