Ndandanda ya Mlungu wa November 22
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 22
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 15 ndime 10-17, ndi bokosi la patsamba 177
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 1-5
Na. 1: 2 Mbiri 3:1-13
Na. 2: Kodi Yehova Anakhululukira Anthu Machimo Chikhristu Chisanayambe pa Maziko Otani? (Aroma 3:24, 25)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimalalikira Kunyumba ndi Nyumba? (rs tsa. 277 ndime 2-5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Mabuku Ogawira M’mwezi wa December. Nkhani yokambirana ndi omvera. Fotokozani zimene zili m’mabukuwo, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza zimene tinganene pogawira mabukuwo.
Mph. 20: “Yesetsani Kucheza ndi Anthu Osakhulupirira Amene Akazi Kapena Amuna Awo Ndi Mboni.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Funsani wofalitsa amene ali pa banja yemwe poyamba anali wosakhulupirira. Kodi mpingo unamuthandiza bwanji kuti ayambe kuchita chidwi ndi choonadi?