Yesetsani Kucheza ndi Anthu Osakhulupirira Amene Akazi Kapena Amuna Awo ndi Mboni
1. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Akhristu onse mumpingo amalakalaka anthu amene akazi kapena amuna awo ndi Mboni ataphunzira choonadi?
1 Kodi mumpingo mwanu muli ofalitsa ena omwe ali ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira? Ngati ndi choncho, n’zachidziwikire kuti ofalitsawo amalakalaka kuti amuna kapena akazi awowo ayambe kulambira koona. Koma si iwo okha amene amalakalaka zimenezi zitachitika. Mpingo wonse umakhala ndi maganizo ngati a Mulungu akuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Ndiye tingatani kuti tizicheza ndi anthu osakhulupirira amene akazi kapena amuna awo ndi ofalitsa a mumpingo mwathu?
2. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kuti tithandize munthu wosakhulupirira?
2 Choyamba, tiyenera kuona zinthu mmene wosakhulupirirayo amazionera. Ambiri mwa anthu amenewa amakonda mabanja awo ndipo amayesetsa kukhala mwamuna kapena mkazi wabwino komanso kholo labwino. Mwina zimene amakhulupirira pa nkhani yachipembedzo ndi zosiyana ndi zimene ifeyo timakhulupirira. N’kutheka kuti samadziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova ndipo zimene amadziwazo anazimva kuchokera kwa anthu amene samadziwa zoona kapena amadana nafe. Ena amakhumudwa chifukwa cha nthawi imene mkazi kapena mwamuna wawo amaigwiritsa ntchito pakulambira yomwe poyamba ankaigwiritsa ntchito posamalira banja lake. Kuzindikira kungatithandize kuchita zinthu ndi munthu wosakhulupirirayo mwachifundo komanso mwaulemu ndiponso kupewa kukhala ndi mantha osayenera tikakumana naye.—Miy. 16:20-23.
3. Kodi njira yabwino kwambiri yokopera munthu wosakhulupirira ndi iti?
3 Muziwasonyeza Chidwi: Njira yoyamba, yomwenso ndi yabwino kwambiri, yokopera munthu wosakhulupirira kuti aphunzire choonadi ndiyo mwa zochita zathu, osati kukambirana naye zokhudza Baibulo. (1 Pet. 3:1, 2) Ndipo njira yabwino yochitira zimenezi ndi kuwasonyeza chidwi. Alongo a mumpingomo angamasonyeze chidwi kwa mkazi amene mwamuna wake ndi Mboni, ndipo abale angachite chimodzimodzi kwa mwamuna amene mkazi wake ndi Mboni. Kodi angachite zimenezi motani?
4. Kodi tingasonyeze bwanji chidwi kwa munthu wosakhulupirira?
4 Ngati simunakumanepo ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirirayo, mungachite zimenezo pambuyo pokambirana ndi m’bale kapena mlongoyo. Musakhumudwe ngati munthuyo sanakulandireni bwino pa ulendo woyamba. Kukhala kwathu aubwenzi komanso kumusonyeza chidwi kungamuthandize kuyamba kuona Mboni za Yehova moyenerera. (Aroma 12:20) Akhristu ena achikulire mwauzimu amaitana anthu osakhulupirira limodzi ndi mabanja awo kuti adzadyere limodzi chakudya, n’cholinga choti adziwane nawo ndiponso kuti athetse chidani chilichonse chimene angakhale nacho. Kenako, wosakhulupirirayo akayamba kumasuka, zimakhala zosavuta kuyamba kukambirana naye nkhani zokhudza Baibulo. Kapena akhoza kuvomera titamuitanira kumisonkhano yathu kuti adzaone zimene mkazi wake amaphunzira. Zingakhale zosavuta kuti avomere chifukwa akudziwana kale ndi anthu ena mumpingomo. Ngakhale atakhala kuti panopa alibe chidwi chodziwa choonadi, mungamuyamikire chifukwa cha zimene amachita pothandiza mkazi wakeyo.
5. Kodi akulu angathandize bwanji munthu wosakhulupirira?
5 Makamaka akulu ndi amene ayenera kuyesetsa kucheza ndi anthu amene mkazi kapena mwamuna wawo ndi Mboni ndiponso ayenera kukhala okonzeka kuchitira umboni ngati mpata utapezeka. Anthu osakhulupirira amene akhala akukana kukambirana nawo nkhani zokhudza Baibulo, akhoza kumvetsera pamene tikuwapatsa chilimbikitso cha m’Malemba atakhala kuti ali m’chipatala kapena akudwala kwambiri. Ngati banja lotereli lakumana ndi vuto linalake, monga imfa ya wachibale, akulu angapemphe munthu wosakhulupirirayo kuti akhalepo pamene iwo akutonthoza ndiponso kulimbikitsa banjalo.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kucheza ndi anthu osakhulupirira amene akazi kapena amuna awo ndi Mboni?
6 Tangoganizani chimwemwe chimene Mkhristu angakhale nacho ngati mkazi kapena mwamuna wake wosakhulupirira ataphunzira choonadi. Zinthu zimenezi zikachitika, Yehova, angelo, ndiponso anthu onse mumpingo amasangalala. (Luka 15:7, 10) Komabe, ngati wosakhulupirirayo sanasonyeze chidwi pa nthawi yoyamba, tingakhalebe osangalala podziwa kuti Yehova amasangalala ndi kuyesetsa kwathu kupitirizabe kumuthandiza, chifukwa iye “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet. 3:9.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Njira yoyamba, yomwenso ndi yabwino kwambiri, yokopera munthu wosakhulupirira kuti aphunzire choonadi ndiyo mwa zochita zathu, osati kukambirana naye zokhudza Baibulo