Ndandanda ya Mlungu wa November 29
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 29
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 15 ndime 18-23, ndi bokosi la patsamba 180a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mbiri 6-9
Na. 1: 2 Mbiri 6:12-21
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Zimazunzidwa? (rs tsa. 278 ndime 2 ndi 3)
Na. 3: Zimene Tiyenera Kuchita Kuti “Tipitirize Kugonjetsa Choipa mwa Kuchita Chabwino” (Aroma 12:21)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: “Kupemphera Ndiponso Kusinkhasinkha N’kofunika Kwa Atumiki Achangu.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze nthawi imene amasinkhasinkha.
Mph. 10: ‘Aliyense Apereke Chopereka kwa Yehova.’ Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2010, masamba 20-21.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa December. Nkhani yokambirana ndi omvera. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani mitu iwiri kapena itatu, ndipo funsani omvera kuti afotokoze mafunso ndiponso malemba amene akhoza kugwiritsa ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse.
[Mawu a M’munsi]
a Mungasankhe kukambirana bokosi kapena ayi.