Kupemphera Ndiponso Kusinkhasinkha N’kofunika kwa Atumiki Achangu
1. Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti apitirize kuika maganizo ake onse pa ntchito yake yofunika kwambiri?
1 Madzulo atsiku lina Yesu anakhalira kuchiritsa odwala ndi kutulutsa ziwanda. Ophunzira ake atam’peza tsiku lotsatira, anamuuza kuti: “Anthu onse akukufunafunani,” ndipo ankamukakamiza kuti apitirize kuchita zozizwitsa. Komabe, Yesu sanalole kuti chilichonse chisokoneze ntchito yake yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino. Iye anayankha kuti: “Tiyeni tipite kwina kumidzi yapafupi, kuti ndikalalikire kumenekonso, pakuti ndicho cholinga chimene ndinabwerera.” Kodi n’chiyani chinathandiza Yesu kuti asatanganidwe ndi zinthu zina? Analawirira m’mawa kudakali mdima kukapemphera ndi kusinkhasinkha. (Maliko 1:32-39) Kodi kupemphera ndiponso kusinkhasinkha kungatithandize bwanji kuti tizilalikira mwachangu?
2. Kodi tingasinkhesinkhe za zinthu ziti kuti tikhalebe achangu mu utumiki?
2 Kodi Tiyenera Kusinkhasinkha za Chiyani? Yesu anaona kuti anthu anali “onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Nafenso tiyenera kuganizira zoti anthu akufunikira kwambiri kumva uthenga wabwino. Tiyenera kuganiziranso kuti tikukhala m’nthawi yofunika kuchita zinthu mwachangu. (1 Akor. 7:29) Tingaganizire za ntchito za Yehova komanso makhalidwe ake, mwayi umene tili nawo wokhala Mboni za Yehova, komanso za chuma chauzimu chamtengo wapatali chimene tachiphunzira m’Mawu a Mulungu chomwe anthu a m’dera lathu sanachidziwebe.—Sal. 77:11-13; Yes. 43:10-12; Mat. 13:52.
3. Kodi tingasinkhesinkhe nthawi yanji?
3 Kodi Tiyenera Kusinkhasinkha Nthawi Yanji? Mofanana ndi Yesu, anthu ena amalawirira m’mawa kuti asinkhesinkhe. Ena amaona kuti zimakhala bwino kusinkhasinkha madzulo asanagone. (Gen. 24:63) Ngakhale titakhala kuti timatanganidwa, tikhoza kupeza nthawi yosinkhasinkha. Ena amachita zimenezi pamene ali pa ulendo. Ena amagwiritsa ntchito nthawi yawo yopuma masana kuti asinkhesinkhe popanda chowasokoneza. Ambiri amaona kuti kusinkhasinkha asanalowe mu utumiki, ngakhale kwa nthawi yochepa chabe, kumawathandiza kulalikira molimba mtima komanso mwachangu.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kusinkhasinkha?
4 Kusinkhasinkha ndiponso kupemphera kudzawonjezera chidwi chathu chofuna kutumikira Yehova, kudzatithandiza kuona kuti kulambira kwathu ndi kofunika kwambiri, ndiponso kudzatilimbikitsa kukhalabe ndi mtima wofuna kupitiriza kulalikira. Mtumiki Wamkulu wa Mulungu, Yesu, anapindula chifukwa chosinkhasinkha, ndipo nafenso tingapindule.