Zilengezo
◼ February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Poyenderanso anthu amene anachita chidwi paulendo woyamba ndiponso anthu amene anafika pa Chikumbutso kapena pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga chanu chikhale kuyambitsa maphunziro a Baibulo.