Ndandanda ya Mlungu wa March 1
MLUNGU WOYAMBIRA MARCH 1
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Rute 1-4
Na. 1: Rute 3:1-13
Na. 2: Mmene Kukhala Achifundo Kumatipindulitsira (Mat. 5:7)
Na. 3: Kodi Chilango cha Uchimo N’chiyani? (rs tsa.149 ndime 2 mpaka 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo. Lengezani tsiku lotsatira limene lasankhidwa kudzayambitsa maphunziro a Baibulo. Fotokozani zokumana nazo zolimbikitsa, funsani wofalitsa kuti afotokoze maulaliki amene wagwiritsa ntchito mogwira mtima m’gawo lanu. M’pempheni kuti achite chitsanzo pogwiritsa ntchito ena mwa mawu oyamba opezeka patsamba 13 pakamutu kakuti “Phunziro la Baibulo Lapanyumba,” m’buku la Kukambitsirana.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Ubwino Wolankhula Motsimikiza mu Utumiki. Kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, patsamba 194 mpaka 196.