Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 22, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 4 mpaka February 22, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi Tera, bambo wa Abulahamu, anali wolambira mafano? [w04 12/1 tsa. 12]
2. Kodi n’chiyani chimene tingati chinachititsa Yoswa kunena mawu a pa Yoswa 24:14, 15, ndipo kodi zimenezi ziyenera kutikhudza motani? [w08 5/15 mas. 17-18 ndime 4-6]
3. Kodi ndi njira imodzi iti imene anthu olambira Baala ndiponso kalambiridwe kawo zinakhalira msampha kwa Aisiraeli? (Owe. 2:3) [w08 2/15 tsa. 27 ndime 2-3]
4. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa kulimba mtima kwa Ehudi pogwiritsa ntchito lupanga? (Owe. 3:16, 21) [w97 3/15 tsa. 31 ndime 4]
5. Kodi zimene Yehova anachita populumutsa Gideoni ndi amuna 300 zimatilimbikitsa bwanji? (Owe. 7:19-22) [w05 7/15 tsa. 16 ndime 8]
6. Zinatheka bwanji kuti mtima wa Yehova ugwidwe chisoni chifukwa cha mavuto a Israeli? (Owe. 10:16) [cl tsa. 254-255 ndime 10-11]
7. Kodi Yefita ankaganiza zopereka munthu ngati nsembe pamene ankanena chowinda chake? (Owe. 11:30, 31) [w05 1/15 tsa. 26 ndime 1]
8. Kodi mphamvu ya Samsoni inkakhaladi m’tsitsi lake? (Owe. 16:18-20) [w05 3/15 tsa. 28 ndime 5-6]
9. Kodi zinthu zochititsa chidwi zimene Samsoni anachita zofotokozedwa pa Oweruza 16:3 zingatithandize bwanji? [w04 10/15 tsa. 15-16 ndime 7-8]
10. Kodi lemba la Oweruza 16:30 likutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya moyo wa munthu? [w90 9/1 tsa. 5 ndime 5; sp tsa. 13-14]