Ndandanda ya Mlungu wa February 22
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 22
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 19-21
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Buku Logawira mu March. Funsani ofalitsa awiri kuti anene zinthu zimene aona kuti n’zothandiza m’bukuli ndiponso maulaliki ogwira mtima amene akhala akuwagwiritsa ntchito pogawira bukuli m’gawo lanu. Aliyense achite chitsanzo kapena ayerekezere zimene anachita pogwiritsa ntchito bukuli poyambitsa phunziro la Baibulo.
Mph. 10: Kuphunzitsa M’njira Yokambirana Kumalimbikitsa Anthu Kumvetsera. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 251 mpaka tsamba 253, ndime 1.
Mph. 10: Tsogolerani Anthu Achidwi ku Gulu la Yehova. Kambiranani ndi omvera ndime zitatu kuyambira pakamutu ka patsamba 99 m’buku la Gulu. Funsani omvera kuti afotokoze zimene anachita potsogolera anthu achidwi ku gulu la Yehova. Funsani wofalitsa amene wapindula chifukwa chakuti amene ankamuphunzitsa Baibulo anamutsogolera kugulu la Yehova.