Ndandanda ya Mlungu wa June 7
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 7
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv Zakumapeto kuyambira pakamutu patsamba 215-218
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 19-21
Na. 1: 2 Samueli 19:11-23
Na. 2: Kodi Mulungu Amaona Bwanji Zifaniziro Zimene Anthu Amagwiritsa Ntchito Polambira? (rs tsa. 437 ndime 1-4)
Na. 3: Njira Zimene Mdyerekezi Amachititsira Anthu Khungu Kuti Asadziwe Choonadi (2 Akor. 4:4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Lalikirani Zomveka Bwino kwa Ena. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 226-229.
Mph. 10: Zosowa za Pampingo.
Mph. 10: Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino—Kugwira Ntchito M’magawo Omwe Anthu Amalankhula Zinenero Zosiyanasiyana. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Gulu, tsamba 107, ndime 1 ndi 2. Mwachidule, funsani woyang’anira utumiki kuti atchule mipingo ya zinenero zina imene imalalikiranso m’gawo lanu. Kodi pali dongosolo lotani limene mipingoyo inagwirizana pofuna kuti aliyense m’gawolo alalikiridwe komanso kuti munthu mmodzi asamalalikiridwe ndi anthu awiri a zinenero zosiyana?