Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 28, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 3 mpaka June 28, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Davide anachita pamaliro a Abineri? (2 Sam. 3:31-34) [w05 5/15 tsa. 17 ndime 6; w06 7/15 tsa. 21 ndime 9-10]
2. Kodi Natani analakwitsa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani sanakanidwe ndi Yehova? (2 Sam. 7:3) [rs tsa. 34 ndime 1]
3. Kodi nkhani yopezeka pa lemba la 2 Samueli 6:1-7 ikutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kumvera? [w05 5/15 tsa. 17 ndime 7]
4. Kodi zimene Davide anachitira Mefiboseti zinasonyeza bwanji kuti anali wokoma mtima, ndipo kodi zimenezi ziyenera kutikhudza bwanji? (2 Sam. 9:7) [w02 5/15 tsa. 19 ndime 5]
5. Kodi tikuphunzira chiyani pa ubwenzi umene unali pakati pa Mfumu Davide ndi Itai yemwe anali Mgiti? (2 Sam. 15:19-22) [w09 5/15 masamba 27 ndi 28]
6. Mwa kugwiritsa ntchito Malemba, kodi tingafotokoze bwanji kuti zimene Ziba ananena zokhudza Mefiboseti zinali zabodza? (2 Sam. 16:1-4) [w02 2/15 masamba 14 ndi 15 ndime 11, mawu a m’munsi]
7. Davide atapempha Barizilai, yemwe panthawiyo anali ndi zaka 80, kuti azikakhala m’bwalo lake, n’chifukwa chiyani Barizilai anauza Davide kuti atenge Chimamu? (2 Sam. 19:33-37) [w07 6/1 tsa. 24 ndime 13]
8. Kodi kudzichepetsa kwa Yehova kunam’kweza bwanji Davide? (2 Sam. 22:36) [w07 11/1 tsa. 5 ndime 2; w04 11/1 tsa. 29]
9. N’chifukwa chiyani Adoniya anayesa kulanda ufumu Davide adakali moyo? (1 Maf. 1:5) [w05 7/1 tsa. 28 ndime 5]
10. N’chifukwa chiyani Yehova anayankha pemphero la Solomo lopempha nzeru ndi kuzindikira? (1 Maf. 3:9) [w05 7/1 tsa. 30 ndime 2]