Ndandanda ya Mlungu wa July 26
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 26
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 15–17
Na. 1: 1 Mafumu 15:1-15
Na. 2: Kodi Ndi Ndani Amene Analimbikitsa Anthu Kuti Azisankha Okha Zochita Popanda Kutsatira Malamulo a Mulungu? (rs tsa. 172 ndime 3–tsa. 173 ndime 1)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Armagedo Iyenera Kuchitika?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Gawo 3. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, patsamba 114, ndime 2 mpaka patsamba 115, ndime 3. Funsani ofalitsa amene ndi achitsanzo chabwino mu mpingo, amene analowapo Sukulu Yophunzitsa Utumiki kapena Sukulu ya Gileadi, kuti afotokoze phindu limene anapeza ndi maphunzirowo. Ngati mu mpingo mwanu mulibe aliyense amene analowapo masukulu amenewa, fotokozani mawu a abale ndi alongo ena opezeka m’mabuku athu okhudza phindu lolowa m’masukulu amenewa.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini mu August. Kukambirana ndi omvera. Kambiranani kwa mphindi imodzi kapena ziwiri nkhani zimene zili m’magaziniwo. Ndiyeno sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu ndipo pemphani omvera kuti atchule mafunso ndi malemba okhudza nkhanizo amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani zitsanzo za mmene angagawirire magazini amenewo.
Mph. 10: “Nzeru Imatsimikizirika Kukhala Yolungama mwa Ntchito Zake.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho.