Ndandanda ya Mlungu wa August 2
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 2
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 10, ndime 9-15 ndi bokosi patsamba 114
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Mafumu 18-20
Na. 1: 1 Mafumu 18:21-29
Na. 2: Kodi Mawu Akuti Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zidzachoka Amatanthauza Chiyani? (Chiv. 21:1)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kupewa Makhalidwe Otani Amene Amasonyeza Mzimu Wodziimira Pawekha? (rs tsa. 173 ndime 2-8)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Njira Zowonjezera Utumiki Wanu—Gawo 4. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 116, ndime 1-4. Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene amathandiza Gulu Lomanga Nyumba za Ufumu kuti afotokoze chimene chimawasangalatsa ndi utumiki umenewu.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zokumana Nazo Poyambitsa Maphunziro a Baibulo. Kukambirana ndi omvera. Fotokozani zimene zachitika m’gawo lanu patsiku lapadera loyambitsa maphunziro a Baibulo. Pemphani omvera kunena zimene akumana nazo. Sonyezani chitsanzo cha chokumana nacho chosangalatsa chimodzi kapena ziwiri. Malizani ndi kusonyeza chitsanzo cha mmene tingayambitsire phunziro pa ulendo woyamba.