Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 30, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya July 5 mpaka August 30, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi kusinkhasinkha pemphero la Solomo lotsegulira kachisi kungatithandize bwanji kumvetsa mmene Yehova alili wapadera? (1 Maf. 8:22-53) w05 7/1 tsa. 30 ndime 3; it-2 tsa. 989 ndime 4]
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Davide anayenda pamaso pa Yehova “ndi mtima woona” ngakhale kuti anachita zolakwa zambiri? (1 Maf. 9:4) [w97 5/1 tsa. 5 ndime 1 ndi 2]
3. Ponena za Solomo, n’chifukwa chiyani mfumukazi ya ku Seba inanena kuti, “Odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu”? (1 Maf. 10:4-8) [w99 11/1 tsa. 20 ndime 5 mpaka 7]
4. Kodi tinganene chiyani pa mfundo yakuti Yehova analamula kuti Abiya aikidwe m’manda mwa mwambo wake? (1 Maf. 14:13) [cl tsa. 244 ndime 11]
5. Kodi n’chiyani chinali chapadera kwambiri ndi nthawi yoyamba imene Eliya anapita kukaonana ndi Ahabu? (1 Maf. 17:1) [w08 4/1 tsa. 19, bokosi]
6. Kodi Eliya anatanthauza chiyani pamene ananena akuti “mukayikakayika kufikira liti?” (1 Maf. 18:21) [w08 1/1 tsa. 19 ndime 3 ndi 4]
7. Malinga ndi mmene nkhani ya Eliya ikusonyezera, n’chifukwa chiyani Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pa atumiki ake? (1 Maf. 19:1-12) [cl mas. 42 ndi 43 ndime 15 ndi 16]
8. N’chifukwa chiyani Naboti anakana kugulitsa Ahabu munda wake wa mpesa, ndipo zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? (1 Maf. 21:3) [w97 8/1 tsa. 13 ndime 18 mpaka 20]
9. Kodi mkazi wa ku Sunemu analolera bwanji kuvutika kuti asamalire Elisa? (2 Maf. 4:13) [w97 10/1 tsa. 30 ndime 6 mpaka 8]
10. N’chifukwa chiyani Elisa anakana mphatso ya Namani? (2 Maf. 5:15, 16) [w05 8/1 tsa. 9 ndime 2]