Ndandanda ya Mlungu wa August 30
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 30
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 9-11
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: “Kodi Mwagwiritsapo Ntchito Tsamba Lomaliza?” Nkhani yokambirana ndi omvera. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili mu nkhaniyi, khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya September 1. Kenako sankhani nkhani imodzi kapena ziwiri za mu Galamukani! ya September ndipo pemphani omvera kuti atchule mafunso ndi malemba amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniyi pogwiritsa ntchito nkhani zimenezi. Khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Galamukani! imeneyi.
Mph. 20: “Mukhoza Kukwanitsa Kulalikira Mwamwayi.”—Gawo 2. Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Kambiranani ndime 9 mpaka 13 ndi bokosi la patsamba 6.