Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu August: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi Dikirani! September: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba womwewo. October: Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?
◼ M’mwezi wa September, oyang’anira dera adzayamba kukamba nkhani ya mutu wakuti “Musamaone Zinthu Zopanda Pake.”