Ndandanda ya Mlungu wa September 6
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 6
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv Zakumapeto. Masamba 219-222.
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 12-15
Na. 1: 2 Mafumu 13:1-11
Na. 2: Njira Zimene Tingalandirire Mzimu Woyera
Na. 3: Kodi Kutchula Dzina la Mulungu Kolondola N’kuti, Yehova Kapena Yahweh, Ndipo N’chifukwa Chiyani Tifunika Kudziwa ndi Kugwiritsa Ntchito Dzinali? (rs-CN tsa. 419 ndime 1–tsa. 421 ndime 7)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Zifukwa Zosonyeza Kuti Ife si Aneneri Onyenga. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 35, ndime 3 mpaka tsamba 36 ndime 2. Khalani ndi chitsanzo chimodzi pogwiritsa ntchito mfundo za patsamba 36 ndi 37.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Funsani mafunso wofalitsa mmodzi kapena awiri achitsanzo chabwino amene atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri. Kodi ntchito yolalikira yasintha bwanji kuchokera pamene iwo anayamba kulalikira? Kodi ntchito ya Ufumu yapita patsogolo motani m’dera lawo komanso padziko lonse? Kodi gulu la Yehova lawathandiza bwanji kupita patsogolo monga olengeza Ufumu?