Mayi Wathanzi Amaberekanso Mwana Wathanzi
1. Kodi makolo anzeru amene akuyembekezera kubereka ayenera kuchita chiyani kuti apewe mavuto okhudzana ndi kubereka?
1 Amayi ambiri amabereka bwinobwino, koma si amayi onse amene zimawayendera bwino pobereka. Choncho, makolo anzeru amene akuyembekezera kubereka amachita zonse zotheka kuti mwana wawo adzabadwe bwinobwino. Mwachitsanzo, iwo amafufuziratu zinthu zimene zimachititsa mavuto amene amatha kukhalapo pobereka. Amaonetsetsanso kuti mayi wapakati akulandira chithandizo choyenerera cha kuchipatala. Ndipo iwo amatsatira zinthu zimene zingachepetse mavuto amenewa. Tiyeni tikambirane bwinobwino zimenezi.
2. Kodi chinthu chachikulu chimene chimayambitsa mavuto kwa mwana ndiponso mayi pobereka n’chiyani?
2 Zinthu Zimene Zimayambitsa Mavuto Pobereka: Chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuti pakhale mavuto kwa mwana ndiponso mayi ndicho kusalandira chithandizo choyenera panthawi imene mayiyo ali woyembekezera. Dokotala wina wa ana anati: “Pamakhala mavuto aakulu ngati mayi salandira chithandizo cha kuchipatala panthawi imene ali woyembekezera.” Iye ananenanso kuti: “Ambiri mwa amayi otere amayembekezera kubereka ana athanzi ndiponso onenepa, koma nthawi zambiri zimenezi sizichitika.” Magazini ina inanena kuti “amayi ambiri amamwalira pobereka” chifukwa chotaya magazi ambiri, chifukwa choti mwana akukanika kutuluka, chifukwa chothamanga magazi, kapenanso chifukwa cha matenda ena. Magaziniyi inanenanso kuti, mavuto amenewa si odetsa nkhawa chifukwa njira zowathetsera n’zosavuta, ndipo “njira zambiri zamakono . . . sizichita kufuna zipangizo zapamwamba kwambiri.”—Journal of the American Medical Women’s Association.
3. Kodi n’chifukwa chiyani mayi woyembekezera ayenera kumapita kusikelo?
3 Njira Yabwino Yothandizira Amayi Ndiponso Ana: Magazini ya UN Chronicle inati: “Mayi wathanzi amaberekanso mwana wathanzi.” Ndipo inanenanso kuti amayi akalandira chithandizo chakuchipatala chochepa kapena akapanda kulandira chithandizo chilichonse pamene ali oyembekezera, pamene akubereka kapena atangobereka kumene, mwana wawo amalandiranso chithandizo chochepa chakuchipatala kapena salandira chithandizo n’komwe. M’mayiko ena n’zovuta kuti mayi woyembekezera apeze chithandizo choyenera chakuchipatala. Mwina angafunike kuyenda ulendo wautali kuti akafike kuchipatala, kapena sangakwanitse kulipira ndalama zofunika kuchipatala. Komabe, ngati zingatheke, mayi woyembekezera ayenera kumapita kusikelo. Zimenezi n’zofunika kwambiri kwa amayi amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, chifukwa Baibulo limanena kuti moyo wa munthu, kuphatikizapo wa mwana wosabadwa, ndi wopatulika.—Eksodo 21:22, 23; Deuteronomo 22:8.
4. Kodi nthawi yoopsa kwambiri kwa mayi woyembekezera ndi iti?
4 Kuchepetsa Mavuto Amene Amakhalapo Pobereka: Nthawi yovuta kwambiri kwa mayi woyembekezera ndi pamene akubereka. Kodi amayi oyembekezera angathandizidwe bwanji kuti moyo wawo usakhale pangozi pa nthawi yovuta imeneyi? Pali zinthu zosavuta kuzitsatira zimene amayi oyembekezera angachite ndipo ayenera kuzichita nthawi idakalipo. Zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka kwa amayi amene salola kuikidwa magazi chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo kapena amene amakana magazi chifukwa choopa matenda.—Machitidwe 15:20, 28, 29.
5. Kodi mayi wanzeru wachikhristu amene akuyembekezera, angatani kuti apewe mavuto obwera chifukwa cha kuchepa kwa magazi m’thupi?
5 Amayi amene salola kuikidwa magazi ayenera kuonetsetsa kuti munthu amene akuwathandizayo, kaya ndi dokotala kapena nesi, ndi wodziwa bwino ntchito yake komanso wakhala akuthandiza anthu popanda kugwiritsa ntchito magazi. Ndiponso amayi oyembekezera ayenera kufufuziratu kuti adziwe ngati dokotala kapena nesi amene adzawathandize pobereka angathe kuwathandiza popanda kuwaika magazi. Mayi wanzeru amapita kuchipatala kuti madokotala akamuone n’cholinga choti akamadzachira adzakhale ndi magazi okwanira. Ngati alibe magazi okwanira, madokotala angamulangize mayiyo kuti azidya zakudya zokhala ndi vitamini B komanso ayironi. Kutsatira malangizo osavuta amenewa kungathandize kupewa mavuto ambiri komanso kuti amayi azikhala athanzi n’kumaberekanso ana athanzi.