Ndandanda ya Mlungu wa August 16
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 16
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 1-4
Na. 1: 2 Mafumu 1:1-10
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Chuma Sichingatibweretsere Chimwemwe Chosatha? (Mlaliki 5:10)
Na 3: Kodi Dzina la Mulungu Limapezeka Pati M’Mabaibulo Amene Anthu Amakonda Kugwiritsa Ntchito Masiku Ano? (rs tsa. 415 ndime 8 mpaka tsa. 417 ndime 8)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Thandizani Wophunzira Wanu Kukhala Wofalitsa. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 78 ndime 3 mpaka kumapeto kwa tsamba 80.
Mph. 10: Thandizani Ena Kuona Phindu la Uthenga Wabwino. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 159. Pemphani omvera kuti afotokoze zinthu zimene anthu ambiri amada nazo nkhawa m’gawo lanu. Apempheni kuti afotokoze mmene tingawathandizire anthuwa tikamalalikira.
Mph. 10: “Chakudya cha pa Nthawi Yoyenera.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ngati mukulidziwa.