Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/10 tsamba 2
  • ‘Chakudya cha pa Nthawi Yoyenera’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Chakudya cha pa Nthawi Yoyenera’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Pulogalamu ya Tsiku la Msonkhano Wapadera wa 2010
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 8/10 tsamba 2

‘Chakudya cha pa Nthawi Yoyenera’

1. Kodi msonkhano wapadera waposachedwapa wathandiza bwanji inuyo komanso anthu ena?

1 Nthawi zambiri tikamaliza tsiku la msonkhano wapadera, timanena kuti: “Msonkhanowu wabwera pa nthawi yake.” Woyang’anira dera wina ananena kuti anthu ena a m’gawo lake atamvera nkhani za tsiku la msonkhano wapadera, ananena kuti akufuna kuwonjezera zimene amachita mu utumiki. Woyang’anira woyendayenda wina anati, “Msonkhanowu unatithandiza kuti tiganizire mofatsa za nthawi imene tili, komanso mmene tikugwiritsira ntchito moyo wathu.” Winanso anati, “Ofalitsa ena ananena kuti msonkhanowu unawathandiza kuti ayambenso kulimbikira ntchito yofunika kwambiri yolalikira.” Kodi inuyo msonkhano wapadera waposachedwapa wakuthandizani bwanji?

2. Kodi msonkhano wapadera wa chaka cha utumiki chikubwerachi udzakhala ndi nkhani zotani?

2 Msonkhano wapadera wa chaka chikubwerachi udzakhalanso wothandiza kwambiri. Mutu wake udzakhala wakuti: “Thawirani kwa Yehova,” ndipo watengedwa pa Salmo 118:8, 9. Pamsonkhanowu padzakambidwa nkhani monga izi: “Kodi Yehova Amakhala Bwanji Malo Achitetezo Champhamvu pa Nthawi ya Nsautso?” “Thandizani Ena Kuthawira M’mapiko a Yehova” “Tsanzirani Yehova Kuti Anthu Ena Azithawira kwa Inu” “Achinyamata, Dalirani Yehova” ndiponso “Yehova Watipatsa Paradaiso Wauzimu Kuti Akhale Malo Athu Othawirapo.”

3. Kodi tidzapindula bwanji tikadzapezeka pamsonkhanowu?

3 Zomwe Mungachite Kuti Mudzapindule: Akangolengeza tsiku la msonkhano wapadera, muyambiretu kukonzekera kuti mudzapezekepo. Muitanenso anthu amene mukuphunzira nawo Baibulo kuti mudzakhale nawo limodzi pamsonkhanowu. Ngati tikufuna “kubereka zipatso mwa kupirira,” tiyenera kukumbukira zimene timamva. (Luka 8:15) Choncho, muzikamvetsera mwatcheru. Muzikalembanso mfundo zazikulu ndiponso malangizo amene mukufuna kuwagwiritsira ntchito pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku komanso mu utumiki wanu. Msonkhanowu ukatha mudzapatule nthawi yoti inuyo ndi anthu a m’banja lanu mudzakambirane mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zimene munaphunzira.

4. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera mwachidwi tsiku la msonkhano wapadera umene ukubwerawu?

4 Mofanana ndi chakudya chokoma komanso chopatsa thanzi, nkhani za pa tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki chikubwerachi zakonzedwa mwachikondi. Komanso mfundo zake anaziganizira mozama. Yehova akudalitseni kuti mudzakhalepo pamsonkhanowu komanso mudzapindule ndi chakudya chauzimu cha panthawi yoyenera chimene wakonzera atumiki ake.—Mat. 24:45.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena