Ndandanda ya Mlungu wa August 23
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 23
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 5-8
Na. 1: 2 Mafumu 6:8-19
Na. 2: Kodi N’chifukwa Chiyani Mabaibulo Ambiri Sagwiritsa Ntchito Dzina Lenileni la Mulungu Kapena Limangopezeka Nthawi Zochepa? (rs tsa. 417 ndime 9 mpaka tsa. 418 ndime 4)
Na. 3: Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Chilakolako cha Thupi Chikhale Mulungu? (Afil. 3:18, 19)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Yambitsani Phunziro la Baibulo pa Ulendo Woyamba mu September. Nkhani yokambirana ndi omvera. M’mwezi wa September tidzagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Tidzayesetse kukambirana ndime imodzi kapena ziwiri ndi mwininyumba pa ulendo woyamba. Kambiranani njira zingapo zimene mungachitire zimenezi. Khalani ndi chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza njira zimenezi.
Mph. 20: “Mukhoza Kukwanitsa Kulalikira Mwamwayi.”—Gawo 1. Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Kambiranani ndime 1 mpaka 8. Khalani ndi chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo za m’nkhaniyi polalikira mwamwayi.