Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 25, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 6 mpaka October 25, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi tikaganizira moyo wa Mfumu Azariya (Uziya) tikuphunzirapo chiyani? (2 Maf. 15:1-6) [w91 7/15 mas. 29-30]
2. Kodi pa lemba la 2 Mafumu 13:14-19 timaphunzirapo chiyani? [w05 8/1 tsa. 11]
3. Kodi Hezekiya anachita pangano ndi dziko la Iguputo? (2 Maf. 18:19-21, 25) [w05 8/1 tsa. 11]
4. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Yehova ‘amakonza’ chifuniro chake? (2 Maf. 19:25) [w99 8/15 tsa. 14 ndime 3]
5. N’chifukwa chiyani Yehova sanakhululukire Yuda? (2 Maf. 24:3, 4) [w05 8/1 tsa. 12]
6. N’chifukwa chiyani lemba la 1 Samueli 16:10, 11 limati Davide anali mwana wa 8 wa Jese, pamene Ezara analemba kuti anali mwana wa 7? (1 Mbiri 2:15) [w02 9/15 tsa. 31]
7. Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha anthu akale a ku Giliyadi? (1 Mbiri 5:10, 18-22) [w05 10/1 p. 9 tsa. 7]
8. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Alevi amene anali olondera zipata? (1 Mbiri 9:26, 27) [w05 10/1 tsa. 9 ndime 8]
9. N’chifukwa chiyani pa 1 Mbiri 11:11 pamanena kuti anthu ophedwa anali 300 pamene lemba la 2 Samueli 23:8, pofotokoza zochita za munthu yemweyo, limanena kuti ophedwa anali 800? [w05-E 10/1 tsa. 10; it-2 tsa. 113]
10. Kodi chinalakwika n’chiyani ndi mmene Davide anakwiyira monga mmene lemba la 1 Mbiri 13:11 limasonyezera? [w05 10/1 tsa. 11]