Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni kapepala kakuti, Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. November: Gawirani kabuku kakuti, Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? ndiponso kakuti Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? December: Gawirani buku lakuti, Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mwapeza ana panyumba gawirani buku lakuti, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ndipo m’mwezi wa January 2011, tidzagawira buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati eninyumba ali nalo kale bukulo, ofalitsa angagawire buku lililonse la masamba 192 lomwe linafalitsidwa chaka cha 1995 chisanafike.
◼ Pa nthawi ya ntchito yapadera mu November, tidzagawira kabuku katsopano kakuti, “Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?” Musaitanitse kabuku kameneka chifukwa mpingo uliwonse tidzautumizira mogwirizana ndi kuchuluka kwa ofalitsa.