Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 27, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya November 1 mpaka December 27, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mawu otamanda Mulungu amene ali m’nyimbo imene Alevi anaimba yolembedwa pa 1 Mbiri 16:34? [w02 1/15 tsa. 11 ndime 6-7]
2. Kodi lemba la 1 Mbiri 22:8 limasonyeza kuti nkhondo zimene Davide anamenya zinali zolakwika, moti n’chifukwa chake Yehova sanafune kuti iye amange nyumba Yake? Fotokozani. [it-2-E tsa. 987 ndime 1]
3. Kodi mfumu Davide inafuna kuti mwana wake adziwe chiyani ponena za Mulungu? (1 Mbiri 28:9) [w08 10/15 tsa. 7 ndime 18]
4. N’chifukwa chiyani kunali koyenera kugwiritsa ntchito zizindikiro za ng’ombe zamphongo pomanga malo oikapo thanki yamkuwa? (2 Mbiri 4:2-4) [w05 12/1 tsa. 19 ndime 3; w98 6/15 tsa. 16 ndime 17]
5. Kodi mu likasa la pangano munkakhala magome awiri okha aja, kapena munkakhalanso zinthu zina? (2 Mbiri 5:10) [w06 1/15 tsa. 31]
6. Kodi Solomo ankatanthauza chiyani pamene ankapempha Yehova kuti azimva mapemphero ochonderera a aliyense “wopemphera atayang’ana nyumba ino”? (2 Mbiri 6:21, 32, 33) [it-1-E tsa. 137 ndime 1]
7. Kodi n’chifukwa chiyani pangano losatha lotchulidwa pa 2 Mbiri 13:5 limatchedwanso kuti “pangano la mchere” malinga ndi mawu a m’munsi? [w05 12/1 tsa. 20 ndime 2; it-2-E tsa. 842 ndime 7]
8. Kodi lemba la 2 Mbiri 17:9, 10 lingagwire ntchito motani pa utumiki wathu? [w09 6/15 tsa. 12 ndime 7]
9. Kodi anthu a Mulungu masiku ano adzachita bwanji mogwirizana ndi 2 Mbiri 20:17? [w03 6/1 mas. 21-22 ndime 14-17]
10. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani ya kudzikuza kwa Mfumu Uziya? (2 Mbiri 26: 15-21) [w99 12/1 tsa. 26 ndime 1-2]