Muzionetsetsa Kuti Mukulalikira Nawo Lamlungu
1. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Paulo ndi anzake anachita ku Filipi?
1 Tsiku lina pa Sabata, Paulo ndi anzake anapezeka mumzinda wa Filipi pa ulendo wawo waumishonale. Popeza kuti Ayuda ambiri a mumzindawo sankagwira ntchito pa tsikuli, palibe amene akanawaimba mlandu chifukwa chosapita kokalalikira pa tsiku limeneli. Komabe iwo ankadziwa kuti Ayuda anali atasonkhana kunja kwa mzindawo n’kumapemphera. Choncho anapezerapo mwayi wokawalalikira. Mayi wina, dzina lake Lidiya, ndi anthu a m’banja lake, anamvetsera uthenga wawo n’kubatizidwa, ndipo Paulo ndi anzake ayenera kuti anasangalala kwambiri. (Mac. 16:13-15) Popeza kuti masiku ano anthu ambiri sagwira ntchito Lamlungu, bwanji nanunso osakonza zoti muzilalikira pa tsiku limeneli?
2. Kodi anthu a Yehova anakumana ndi mavuto otani kuti akhale ndi ufulu wolalikira Lamlungu popanda kuvutitsidwa?
2 Kupeza Ufulu Wolalikira Lamlungu: M’chaka cha 1927, anthu a Yehova analimbikitsidwa kuti aziyesetsa kulalikira Lamlungu lililonse. Koma atangoyamba kuchita zimenezi, anthu sanakondwere nazo. Ku America, abale ndi alongo ambiri anaimbidwa milandu yolalikira Lamlungu, kusokoneza mtendere ndi kugulitsa malonda popanda chilolezo. Koma anthu a Yehova sanabwerere m’mbuyo. M’ma 1930 anakonza magulu akuluakulu aulaliki. Ofalitsa a mipingo ingapo yoyandikana ankasonkhana pamodzi n’kulalikira gawo limodzi. Nthawi zina, akuluakulu a boma amagwira ofalitsa ambiri, moti amangowasiya. Kodi mumayamikira kuti abalewo anadzipereka kwambiri kuti tikhale ndi ufulu wolalikira Lamlungu popanda wina kutivutitsa?
3. N’chifukwa chiyani Lamlungu ndi tsiku labwino kulalikira?
3 Tsiku Labwino Kwambiri Kulalikira: Anthu ambiri sapita kuntchito Lamlungu ndipo nthawi zambiri amangokhala phee! pakhomo. Anthu ena amene amakonda zopemphera sangakane kukambirana nawo za Mulungu pa tsikuli. Ngati timachita misonkhano ya mpingo Lamlungu, ndiye kuti timakhala titavala kale zovala zoyenera kulowa nazo mu utumiki. Ndiye bwanji osakonza zolowa mu utumiki wakumunda misonkhano isanayambe kapena itatha? Komanso mukhoza kutenga kachakudya pang’ono ngati kuli kofunika.
4. N’chifukwa chiyani tingakhale osangalala tikamalalikira Lamlungu kwa maola angapo?
4 Tikamalowa mu utumiki wakumunda Lamlungu kwa maola angapo, tikhoza kutsalabe ndi nthawi yopuma yokwanira. Ndipo tizipuma tili okhutira chifukwa tachita utumiki wopatulika. (Miy. 19:23) Tingasangalalenso kwambiri ngati titapeza munthu amene angamvetsere uthenga wathu ngati Lidiya.