Ndandanda ya Mlungu wa July 18
MLUNGU WOYAMBIRA JULY 18
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 10 ndime 1-10 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 74–78 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 77:1-20 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Njira Zimene Tingatsutsire Mdyerekezi—Yak. 4:7 (Mph. 5)
Na. 3: Ufumu wa Mulungu Udzayeretsa Dzina la Yehova—rs tsa. 376 ndime 3-5 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Gwiritsani Ntchito Mafunso Kuti Muziphunzitsa Mogwira Mtima: Gawo 3. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 239. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri zopezeka m’nkhaniyi.
Mph. 10: “Muzisonyeza Ena ‘Chifundo Chachikulu.’” Mafunso ndi mayankho.
Mph. 10: Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti. (Afil. 1:10) Funsani m’bale mmodzi kapena awiri omwe ndi mitu ya mabanja. Akhale abale amene amagwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse ndiponso amagwira ntchito yolembedwa kapena amene ali ndi udindo waukulu wosamalira banja. Kodi amapeza bwanji nthawi yochitira utumiki? Kodi kugwira nawo ntchito yolalikira nthawi zonse kwawathandiza bwanji iwowo ndiponso mabanja awo?
Nyimbo Na. 25 ndi Pemphero