Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/11 tsamba 2-3
  • Muzilemba Malipoti Molondola N’kuwapereka Mwamsanga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilemba Malipoti Molondola N’kuwapereka Mwamsanga
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 8/11 tsamba 2-3

Muzilemba Malipoti Molondola N’kuwapereka Mwamsanga

1. Kodi timamva bwanji tikamva nkhani zolimbikitsa zimene zikuchitika mu utumiki wakumunda?

1 Tonsefe timasangalala kwambiri tikamamva za zinthu zabwino zimene zikuchitika pa ntchito yathu yolalikira uthenga wa Ufumu. (Onani Miyambo 25:25.) Petulo atamaliza kukamba nkhani yogwira mtima kwambiri pa Pentekosite, chiwerengero cha ophunzira chinawonjezereka ndi “anthu pafupifupi 3,000.” (Mac. 2:41) Patangopita nthawi yochepa, chiwerengerochi chinawonjezerekanso n’kufika anthu “pafupifupi 5,000.” (Mac. 4:4) Kunena zoona, Akhristu a m’nthawi ya atumwi analimbikitsidwa kwambiri kumva za zinthu zosangalatsa zimenezi. Masiku ano, nafenso timasangalala tikamva nkhani zolimbikitsa.

2. Kodi chimafunika n’chiyani kuti tikhale ndi lipoti lolondola?

2 Timasangalala kwambiri tikamva kuti abale athu zinthu zikuwayendera pa ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse. Monga tikudziwa, August ndi mwezi womaliza wa chaka chautumiki ndipo pa nthawi imeneyi, pamakhala ntchito yaikulu yosonkhanitsa malipoti. Chifukwa cha zimenezi, wofalitsa Ufumu aliyense ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi dongosolo. Kodi inuyo mumapereka malipoti anu mofulumira mwezi uliwonse?

3. Kodi kupereka malipoti olondola kumatithandiza bwanji ifeyo komanso gulu la Yehova?

3 Timanyadira kwambiri kumva kuti gulu la Yehova likuwonjezereka. Komanso malipoti amathandiza kwambiri kuti gulu lidziwe mmene ntchito ikupitira patsogolo padziko lonse. Ndiponso, gulu limafuna kudziwa ngati pakufunika thandizo linalake kapena ngati pakufunika mabuku ena atsopano komanso kuti akufunika ochuluka bwanji. Akulu mu mpingo uliwonse amagwiritsa ntchito malipoti a utumiki wakumunda kuti adziwe ngati pakufunika kusintha zina ndi zina. Komanso, lipoti lolondola limatilimbikitsa tonsefe kuonanso mmene tikuchitira utumiki wathu, n’kuona ngati tikufunika kusintha zina ndi zina.

4. Kodi ndi dongosolo liti mumpingo, limene wofalitsa aliyense komanso akulu angatsatire pofuna kuti malipoti azitumizidwa molondola ku ofesi ya nthambi mwezi uliwonse?

4 Wofalitsa aliyense adziwe kuti ndi udindo wake kupereka malipoti a utumiki wakumunda mwamsanga mwezi uliwonse. Choncho, wofalitsa angaponye malipoti ake m’bokosi pa Nyumba ya Ufumu ngati wangofuna kutero kapena ngati walephera kupereka malipotiwo kwa woyang’anira kagulu kake ka utumiki wakumunda. Mlembi ayenera kuchotsa malipoti onse amene aponyedwa m’bokosi mwezi uliwonse. Woyang’anira kagulu ka utumiki wakumunda ayenera kuonetsetsa kuti watolera mofulumira malipoti onse a gulu lake ndipo wawapereka mwachangu kwa mlembi. Wofalitsa komanso mpainiya aliyense ayenera kuonetsetsa kuti wapereka malipoti ake mofulumira mwezi uliwonse. Woyang’anira kagulu ka utumiki amakhala tcheru kuti athandize anthu amene salowalowa mu utumiki. Pa chifukwa chimenechi, mwezi uliwonse, woyang’anira kagulu ka utumiki ayenera kukumbutsa ofalitsa za mmene angalembere komanso kutumiza malipoti. Iye angachite zimenezi pa tsiku lomaliza limene achita msonkhano wa utumiki wakumunda mwezi umenewo, kapena pa nthawi ina imene angasankhe.

5. Kodi wofalitsa aliyense angathandize bwanji kuti lipoti lizikhala lolondola, nanga kasilipi ka Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) kangathandize bwanji kuti tikwanitse kuchita zimenezi?

5 Kodi Ofalitsa Angathandize Bwanji Kuti Malipoti Azikhala Olondola? Kuti malipoti akhale olondola, onetsetsani kuti mwatumiza maola okhawo amene mwatha mukulalikira, osati ndi maminitsi omwe. Ofalitsa okhawo amene adwala kwa nthawi yaitali kapena ndi olumala moti sangathe kuyenda ndipo avomerezedwa ndi Komiti ya Utumiki ya Mpingo, ndi amene angaloledwe kupereka maminitsi 15 amene alalikira monga lipoti lawo la mwezi. Ngati wofalitsa ali ndi maminitsi osakwana ola, angawasunge kuti adzawaphatikize pa maola a mwezi wotsatira. Nthawi iliyonse imene mwalowa mu utumiki wakumunda, mungachite bwino kwambiri kumalemba nthawi imene mwalalikira, mabuku kapena magazini amene mwagawira komanso maulendo obwereza amene mwachita. Zimenezi zidzathandiza kuti musamavutike kuwonkhetsa maola anu pa mapeto pa mwezi. Komanso zidzathandiza kuti musamangolota maola amene mukuganiza kuti mwathera mu utumiki. Kasilipi ka Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) kamathandiza kwambiri kuti musunge bwino maola enieni amene mwathera mu utumiki.

6. Kodi tingawerengere motani ulendo wobwereza?

6 Kodi Tingawerengere Motani Ulendo Wobwereza? Timawerengera ulendo wobwereza ngati takambirana ndi munthu yemwe tinakambirana naye pa ulendo woyamba. Tingawerengerenso maulendo obwereza komanso maola tikapereka magazini kwa anthu amene nthawi zonse timawapatsa magazini, ngati tikulalikira kachiwiri pa telefoni kwa munthu amene tinamulalikirapo m’mbuyomu, kapena ngati talembera kalata munthu amene tinamulalikirapo m’mbuyomu. Tingawerengerenso ulendo wobwereza nthawi iliyonse imene tachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba. Nambala yolondola ya maphunziro a Baibulo onse amene mwachititsa m’mwezi umodzi iyenera kulembedwa m’bokosi loyenera, m’munsi chakumanja pa kasilipi ka Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4).

7. Kodi timamva bwanji tikamachita zinthu mogwirizana ndi dongosolo la gulu?

7 Wofalitsa aliyense amene akuchita zinthu mofunitsitsa komanso mogwirizana ndi dongosolo la gulu limene takambiranali, ayenera kukhala wosangalala podziwa kuti akuthandiza kuti Mboni za Yehova zizikhala ndi lipoti lolondola pa ntchito imene ikuchitika padziko lonse imeneyi. (Yerekezerani ndi Ezekieli 9:11.) Ndiyetu tiyeni tonse tiyesetse kumapereka malipoti olondola komanso pa nthawi yake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena