Ndandanda ya Mlungu wa September 26
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 26
Nyimbo Na. 3 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 13 ndime 9-17 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Salimo 142-150 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 144:1–145:4 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira M’zaka 100 Zoyambirira?—rs tsa. 381 ndime 2 mpaka 4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Sitiyenera ‘Kuchita Zinthu Mokondera?—Yak. 2:1-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Kambiranani nkhani yakuti, “Njira Ina Imene Tingagwiritsire Ntchito Kabuku ka Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?” Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro Loweruka pa October 1. Limbikitsani onse kudzagwira nawo ntchitoyi.
Mph. 10: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambirana. Phatikizanipo mfundo zopezeka mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2005, tsamba 8.
Mph. 15: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa October. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, tchulani nkhani zina zimene zingakhale zogwira mtima m’gawo lanu. Kenako, sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu, ndipo pemphani omvera kuti anene mafunso ndi malemba a mu iliyonse ya nkhanizi, amene tingagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Popeza magazini ya Galamukani! ya October idzakhala yapadera, pemphani omvera kuti afotokoze anthu amene ingawafike pamtima ndiponso zimene tingachite kuti tigawire anthu ambiri magaziniyi. Chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero