Ndandanda ya Mlungu wa November 28
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 28
Nyimbo Na. 35 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 16 ndime 7-14 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Nyimbo ya Solomo 1-8 (Mph. 10)
Na. 1: Nyimbo ya Solomo 1:1–17 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amanena Kuti Masiku Otsiriza Anayamba mu 1914?—rs tsa. 266 ndime 2 mpaka tsa. 267 ndime 1 (Mph. 5)
Na. 3: Tingachite Chiyani kuti Anthu Ena Azitilemekeza? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa December. Limbikitsani onse kuti ayambitse maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: “Khalidwe Lofunika Kwambiri la Mphunzitsi Wabwino.” Mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene chikondi chomwe munthu amene anawaphunzitsa Baibulo anawasonyeza chinawathandizira kupita patsogolo mwauzimu.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini m’Mwezi wa December. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, fotokozani nkhani zimene zili m’magaziniwo zomwe zingakhale zogwira mtima kwa athu a m’gawo lanu. Kenako pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso okopa chidwi amene angafunse ndiponso malemba amene angawerenge. Chitani chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! ndipo ngati nthawi ilipo fotokozaninso nkhani imodzi m’magaziniyi. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero