Ndandanda ya Mlungu wa December 12
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 12
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 17 ndime 1-9 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 6-10 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 6:1-13 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Padutse Nthawi Yaitali Chonchi Asanawononge Oipa?—rs tsa. 268 ndime 2 mpaka 4 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Chikondi Sichitha?—1 Akor. 13:8; 1 Yoh. 4:8 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2012. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Pogwiritsa ntchito ndandanda ya 2012, kambiranani mfundo zimene mukuona kuti zingathandize kwambiri mpingo wanu. Fotokozani udindo wa mlangizi wothandiza. Limbikitsani onse kuchita khama kukwaniritsa mbali zawo, kutenga nawo mbali pa mfundo zazikulu, komanso kugwiritsa ntchito malangizo ochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki amene amaperekedwa mlungu uliwonse.
Mph. 15: “Tizikhala Okonzeka Kulalikira Nthawi Zonse.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 2, funsani wofalitsa amene amachita ulaliki wamwamwayi mogwira mtima kuti afotokoze mmene amakonzekerera komanso afotokoze chokumana nacho chosangalatsa.
Nyimbo Na. 24 ndi Pemphero