Ndandanda ya Mlungu wa January 9
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 9
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 18 ndime 10-18 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yesaya 29-33 (Mph. 10)
Na. 1: Yesaya 30:15-26 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu Analengedwa Kuti Azikhala Ndi Moyo Nthawi Yochepa, Kenako N’kufa?—rs tsa. 291 ndime 2-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Anthu Opanda Ungwiro Angayeretse Bwanji Dzina la Yehova?—Mat. 6:9 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Muzilalikira Anthu Amene Amalankhula Chinenero China. Nkhani yochokera patsamba 2 la kabuku ka Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito kabukuka.
Mph. 10: Umboni Wakuti Baibulo Ndi Louziridwa Ndi Mulungu. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 54 ndime 3, mpaka tsamba 58 ndime 2.
Mph. 10: “Muziponya Nkhonya Zanu Mwanzeru.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 2, funsani mwachidule woyang’anira utumiki kuti afotokoze malo amene mungapeze anthu ambiri ndiponso nthawi yake mkati mwa mlungu, m’gawo la mpingo wanu.
Nyimbo Na. 115 ndi Pemphero